Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Psalms 150 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

1Tamandani Yehova.Tamandani Mulungu mʼmalo ake opatulika;mutamandeni ku thambo lake lamphamvu.

2Mutamandeni chifukwa cha machitidwe ake amphamvu;mutamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana.

3Mutamandeni poyimba malipenga,mutamandeni ndi pangwe ndi zeze.

4Mutamandeni ndi matambolini ndi kuvina,mutamandeni ndi zingwe ndi zitoliro.

5Mutamandeni ndi ziwaya zolira za malipenga,mutamandeni ndi ziwaya zolira kwambiri.

6Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Yehova.Tamandani Yehova.

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]