Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 12 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Nyimbo za Mayamiko

1Tsiku limenelo aliyense wa inu adzati:“Ndikukuyamikani, Inu Yehova;chifukwa ngakhale munandipsera mtima,mkwiyo wanu wachoka,ndipo mwanditonthoza.

2Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga;ndidzamudalira ndipo sindidzachita mantha.Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;Iye wakhala chipulumutso changa.”

3Mudzakondwera popeza Yehovaali ngati chitsime cha chipulumutso chanu.

4Tsiku limenelo mudzati:“Yamikani Yehova, tamandani dzina lake;mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu,ndipo mulalike kuti dzina lake ndi lopambana.

5Imbirani Yehova, pakuti wachita ntchito zazikulu;zimenezi zidziwike pa dziko lonse lapansi.

6Fuwulani ndi kuyimba mwachimwemwe, inu anthu a ku Ziyoni;pakuti Woyerayo wa Israeli ndi wamkulu pakati panu.”

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]