Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Psalms 128 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1Odala ndi onse amene amaopa Yehova,amene amayenda mʼnjira zake.

2Udzadya chipatso cha ntchito yako;madalitso ndi chuma zidzakhala zako.

3Mkazi wako adzakhala ngati mpesa woberekamʼkati mwa nyumba yako;ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivikuzungulira tebulo lako.

4Ameneyu ndiye munthu wodalitsidwaamene amaopa Yehova.

5Yehova akudalitse kuchokera mʼZiyonimasiku onse a moyo wako;uwone zokoma za Yerusalemu,

6ndipo ukhale ndi moyo kuti udzaone zidzukulu zako.Mtendere ukhale ndi Israeli.

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]