Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Psalms 129 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1“Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,”anene tsono Israeli;

2“Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,koma sanandipambane.

3Anthu otipula analima pa msana pangandipo anapangapo mizere yayitali:

4Koma Yehova ndi wolungama;Iye wandimasula ku zingwe za anthu oyipa.”

5Onse amene amadana ndi Ziyoniabwezedwe pambuyo mwamanyazi.

6Akhale ngati udzu womera pa denga la nyumba,umene umafota usanakule;

7sungadzaze manja a owumwetakapena manja a omanga mitolo.

8Odutsa pafupi asanene kuti,“Dalitso la Yehova lili pa inu;tikukudalitsani mʼdzina la Yehova.”

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]