Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Psalms 127 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Salimo la Solomoni.

1Yehova akapanda kumanga nyumba,omanga nyumbayo agwira ntchito pachabe.Yehova akapanda kulondera mzinda,mlonda akanangolondera pachabe.

2Mumangodzivuta nʼkulawirira mmamawandi kusagona msanga madzulo,kuvutikira chakudya choti mudye,pakuti Iye amapereka tulo kwa amene amawakonda.

3Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova,ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.

4Ana a pa unyamata ali ngati mivi mʼmanjamwa munthu wankhondo.

5Wodala munthuamene motengera mivi mwake mwadzaza.Iwo sadzachititsidwa manyazipamene alimbana ndi adani awo pa zipata.

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]