Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Psalms 126 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1Yehova atabwezera akapolo ku Ziyoni,tinali ngati amene akulota.

2Pakamwa pathu panadzaza ndi kuseka;malilime athu ndi nyimbo zachimwemwe.Pamenepo kunanenedwa pakati pa anthu kuti,“Yehova wawachitira zinthu zazikulu.”

3Yehova watichitira zinthu zazikulu,ndipo tadzazidwa ndi chimwemwe.

4Tibwezereni madalitso athu, Inu Yehova,monga mitsinje ya ku Negevi.

5Iwo amene amafesa akulira,adzakolola akuyimba nyimbo zachimwemwe.

6Iye amene amayendayenda nalira,atanyamula mbewu yokafesa,adzabwerera akuyimba nyimbo zachimwemwe,atanyamula mitolo yake.

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]