Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Psalms 125 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1Amene amadalira Yehova ali ngati phiri la Ziyoni,limene silingagwedezeke koma ndi lokhala mpaka muyaya.

2Monga mapiri azungulira Yerusalemu,momwemonso Yehova azungulira anthu akekuyambira tsopano mpaka muyaya.

3Ndodo yaufumu ya anthu oyipa sidzakhalapa dziko limene lapatsidwa kwa anthu olungama,kuti anthu olungamawoangachite nawonso zoyipa.

4Yehova chitirani zabwino amene ndi abwino,amene ndi olungama mtima

5Koma amene amatembenukira ku njira zokhotakhota,Yehova adzawachotsa pamodzi ndi anthu ochita zoyipa.Mtendere ukhale pa Israeli.

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]