Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Psalms 124 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1Akanapanda kukhala mbali yathu Yehova,anene tsono Israeli,

2akanapanda kukhala mbali yathu Yehova,potiwukira anthuwo,

3iwo atatipsera mtima,akanatimeza amoyo;

4chigumula chikanatimiza,mtsinje ukanatikokolola,

5madzi a mkokomoakanatikokolola.

6Atamandike Yehova,amene sanalole kuti tikhale chakudya cha mano awo.

7Moyo wathu wawonjoka ngati mbalameyokodwa mu msampha wa mlenje;msampha wathyoka,ndipo ife tapulumuka.

8Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehovawolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]