Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Job 25 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Mawu a Bilidadi

1Apo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti,

2“Ulamuliro ndi kuopsa ndi za Mulungu,Iye amakhazikitsa bata mu ufumu wake kumwambako.

3Kodi magulu ake ankhondo nʼkuwerengeka?Kodi kuwala kwake sikuwalira ndani?

4Kodi munthu angakhale bwanji wolungama pamaso pa Mulungu?Kodi munthu wobadwa mwa mayi angakhale wangwiro?

5Ngati mwezi sutha kuwala kwenikweni,ndipo nyenyezi sizitha kuwala pamaso pake,

6nanji tsono munthu amene ali ngati mphutsi,mwana wa munthu amene ali ngati nyongolotsi!”

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]