Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Psalms 6 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Molingana ndi seminiti. Salimo la Davide.

1Inu Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu,kapena kundilanga mu ukali wanu.

2Ndichitireni chifundo Inu Yehova, pakuti ndalefuka;Inu Yehova chiritseni, pakuti mafupa anga ali pa ululu waukulu.

3Moyo wanga uli pa mazunzo aakulu.Mpaka liti, Inu Yehova, mpaka liti?

4Tembenukani Inu Yehova, ndipo mundilanditse;pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.

5Palibe amene amakukumbukirani pamene wamwalira;Amakutamandani ndani ali ku manda?

6Ine ndatopa ndi kubuwula;usiku wonse pa bedi panga pamadzaza ndi misozi yanga;ndimanyowetsa pogona panga ndi misozi.

7Maso anga atupa chifukwa cha chisoni;akulephera kuona chifukwa cha adani anga.

8Chokani kwa ine inu nonse amene mumachita zoyipa,pakuti Yehova wamva kulira kwanga.

9Yehova wamva kupempha kwanga kofuna chifundo;Yehova walandira pemphero langa.

10Adani anga onse adzachita manyazi ndipo adzakhala ndi mantha;adzabwerera msangamsanga mwa manyazi.

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]