Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Psalms 7 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Sigioni wa Davide, amene anayimbira Yehova zokhudza Kusi, wa fuko la Benjamini.

1Inu Yehova Mulungu wanga, Ine ndikuthawira kwa Inu;pulumutseni ndi kundilanditsa kwa onse amene akundithamangitsa,

2mwina angandikadzule ngati mkango,ndi kundingʼamba popanda wondipulumutsa.

3Inu Yehova Mulungu wanga,ngati ndachita izi ndipo ndapezeka wolakwa,

4ngati ndachita zoyipa kwa iye amene ndili naye pa mtendere,kapena popanda chifukwa ndalanda mdani wanga,

5pamenepo lolani adani anga andithamangitse ndi kundipitirira,lolani kuti moyo wanga aupondereze pansindipo mundigoneke pa fumbi.Sela

6Nyamukani Yehova, mu mkwiyo wanu;nyamukani kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga.Dzukani Mulungu wanga, lamulirani chilungamo chanu.

7Lolani gulu la anthu a mitundu ina lisonkhane mokuzungulirani.Alamulireni muli kumwambako;

8Yehova aweruzeni anthu a mitundu inayo.Ndiweruzeni Yehova, monga mwa chilungamo changa,monga mwa moyo wanga wangwiro, Inu Wammwambamwamba.

9Inu Mulungu wolungama,amene mumasanthula maganizo ndi mitima,thetsani chiwawa cha anthu oyipandipo wolungama akhale motetezedwa.

10Chishango changa ndi Mulungu Wammwambamwamba,amene amapulumutsa olungama mtima.

11Mulungu amaweruza molungama,Mulungu amene amaonetsa ukali wake tsiku ndi tsiku.

12Ngati munthu satembenuka,Mulungu adzanola lupanga lake,Iye adzawerama ndi kukoka uta.

13Mulungu wakonza zida zake zoopsa;Iye wakonzekera mivi yake yoyaka moto.

14Taonani, munthu woyipa amalingalira zoyipa zokhazokha nthawi zonse.Zochita zake ndi zosokoneza ndi zovutitsa anthu ena.

15Iye amene akumba dzenje ndi kulizamitsaamagwera mʼdzenje limene wakumbalo.

16Mavuto amene amayambitsa amamubwerera mwini;chiwawa chake chimatsikira pa mutu wake womwe.

17Ine ndidzayamika Yehova chifukwa cha chilungamo chake;ndipo ndidzayimba nyimbo zamatamando pa dzina la Yehova Wammwambamwamba.

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]