Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Psalms 11 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

1Mwa Yehova ine ndimathawiramo.Nanga mungathe bwanji kunena kwa ine kuti,“Thawira ku phiri lako ngati mbalame.

2Pakuti taona oyipa akunga mauta awo;ayika bwino mivi yawo pa zingwe za uta,pobisala pawo kuti alaseolungama mtima.

3Tsono ngati maziko awonongeka,olungama angachite chiyani?”

4Yehova ali mʼNyumba yake yoyera;Yehova ali pa mpando wake waufumu kumwamba.Iye amayangʼanitsitsa ana a anthu;maso ake amawayesa.

5Yehova amayesa olungama,koma moyo wake umadana ndi oyipa,amene amakonda zachiwawa.

6Iye adzakhuthulira pa oyipamakala amoto ndi sulufule woyaka;mphepo yotentha idzakhala yowayenera.

7Pakuti Yehova ndi wolungama,Iye amakonda chilungamo;ndipo anthu olungama adzaona nkhope yake.

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]