Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Psalms 12 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe seminiti. Salimo la Davide.

1Thandizeni Yehova pakuti palibe munthu wokhulupirika;okhulupirika akusowa pakati pa anthu.

2Aliyense amanamiza mʼbale wake;ndi pakamwa pawo pabodza amayankhula zachinyengo.

3Inu Yehova tsekani milomo yonse yachinyengondi pakamwa paliponse podzikuza.

4Pakamwa pamene pamati, “Ife tidzapambana ndi kuyankhula kwathu;pakamwapa ndi pathupathu, tsono mbuye wathu ndani?”

5“Chifukwa cha kuponderezedwa kwa anthu opanda mphamvundi kubuwula kwa anthu osowa,Ine ndidzauka tsopano,” akutero Yehova,“Ndidzawateteza kwa owazunza.”

6Ndipo mawu a Yehova ndi angwiromonga siliva oyengedwa mʼngʼanjo yadothi,oyengedwa kasanu nʼkawiri.

7Inu Yehova mudzatitchinjiriza ndipomudzatiteteza kwa anthu otere kwamuyaya.

8Oyipa amangoyendayenda ponseponseanthu akamayamikira zochita zawo.

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]