Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Psalms 15 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Salimo la Davide.

1Yehova, ndani angathe kukhala mʼmalo anu opatulika?Kodi ndani angathe kukhala mʼphiri lanu loyera?

2Munthu wa makhalidwe abwino,amene amachita zolungama,woyankhula choonadi chochokera mu mtima mwake,

3ndipo mʼkamwa mwake simutuluka mawu osinjirira,amene sachitira choyipa mnansi wakekapena kufalitsa mbiri yoyipa ya munthu mnzake,

4amene sapereka ulemu kwa munthu woyipa.Koma amalemekeza amene amaopa Yehova,amene amakwaniritsa zomwe walonjezangakhale pamene zikumupweteka,

5amene amakongoletsa ndalama zake popanda chiwongoladzanjandipo salandira chiphuphu pofuna kutsutsa anthu osalakwa.Iye amene amachita zinthu zimenezisadzagwedezeka konse.

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]