Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Psalms 14 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

1Chitsiru chimati mu mtima mwake,“Kulibe Mulungu.”Oterewa ndi oyipa ndipo ntchito zawo ndi zonyansa;palibe amene amachita zabwino.

2Yehova kumwamba wayangʼana pansi,kuyangʼana anthu onsekuti aone ngati alipo wina wanzeru,amene amafunafuna Mulungu.

3Onse atembenukira kumbali,onse pamodzi asanduka oyipa;palibe amene amachita zabwino,palibiretu ndi mmodzi yemwe.

4Kodi anthu ochita zoyipawa sadziwa chilichonse?Akudya anthu anga ngati chakudya chawondipo satamanda Yehova?

5Awo ali apowo, agwidwa ndi mantha aakulu,pakuti Mulungu ali mʼgulu la olungama.

6Inu ochita zoyipa mumalepheretsa chikonzero cha anthu osauka,koma Yehova ndiye pothawirapo pawo.

7Ndithu, chipulumutso cha Israeli chidzachokera ku Ziyoni!Pamene Yehova abwezeretsa ufulu wa anthu ake,Yakobo akondwere ndipo Israeli asangalale!

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]