Side by side with the Father's Heart Bible™ Ndakatulo ya Davide, pamene iyeyo anali mʼphanga. Pemphero.
1Ndikulirira Yehova mofuwula;ndikukweza mawu anga kwa Yehova kupempha chifundo.
2Ndikukhuthula madandawulo anga pamaso pake;ndikufotokoza za masautso anga pamaso pake.
3Pamene mzimu wanga walefuka mʼkati mwanga,ndinu amene mudziwa njira yanga.Mʼnjira imene ndimayendamoanthu anditchera msampha mobisa.
4Yangʼanani kumanja kwanga ndipo onani;palibe amene akukhudzika nane.Ndilibe pothawira;palibe amene amasamala za moyo wanga.
5Ndilirira Inu Yehova;ndikuti, “Ndinu pothawirapo panga,gawo langa mʼdziko la anthu amoyo.”
6Mverani kulira kwangapakuti ndathedwa nzeru;pulumutseni kwa amene akundithamangitsapakuti ndi amphamvu kuposa ine.
7Tulutseni mʼndende yangakuti nditamande dzina lanu.Ndipo anthu olungama adzandizungulirachifukwa cha zabwino zanu pa ine.