Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Psalms 3 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Salimo la Davide. Atathawa mwana wake Abisalomu.

1Inu Yehova, achulukadi adani anga!Achulukadi amene andiwukira!

2Ambiri akunena za ine kuti,“Mulungu sadzamupulumutsa.”Sela

3Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza,Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula.

4Kwa Yehova, Ine ndilira mofuwulandipo Iye amandiyankha kuchokera ku phiri lake loyera.Sela

5Ine ndimagona ndi kupeza tulo;ndimadzukanso chifukwa Yehova amandichirikiza.

6Sindidzaopa adani anga osawerengeka ameneabwera kulimbana nane kuchokera ku madera onse.

7Dzukani, Inu Yehova!Pulumutseni, Inu Mulungu wanga.Akantheni adani anga onse pa msagwada;gululani mano a anthu oyipa.

8Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.Madalitso akhale pa anthu anu.Sela

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]