Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Psalms 137 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

1Mʼmbali mwa mitsinje ya ku Babuloni tinakhala pansi ndi kulirapamene tinakumbukira Ziyoni.

2Kumeneko, pa mitengo ya misondozitinapachika apangwe athu,

3pakuti anthu otigwira ukapolo anatipempha kuti tiyimbe nyimbo.Otizunza athu anafuna nyimbo zachisangalalo;iwo anati, “Tiyimbireni imodzi mwa nyimbo za ku Ziyoni!”

4Tingayimbe bwanji nyimbo za Yehovamʼdziko lachilendo?

5Ndikakuyiwala iwe Yerusalemu,dzanja langa lamanja liyiwale luso lake.

6Lilime langa limamatire ku nkhama za mʼkamwa mwangandikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu,ngati sindiyesa iwechimwemwe changa chachikulu.

7Kumbukirani, Inu Yehova, zimene Aedomu anachitapa tsiku limene Yerusalemu anagonja.Iwowo anafuwula kuti, “Mugwetseni pansi, mugwetseni pansimpaka pa maziko ake!”

8Iwe mwana wa mkazi wa Babuloni, woyenera kuwonongedwa,wodalitsika ndi yemwe adzakubwezerapa zimene watichitira.

9Amene adzagwira makanda akondi kuwakankhanthitsa pa miyala.

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]