Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Psalms 138 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Salimo la Davide.

1Ndidzakuyamikani Yehova ndi mtima wanga wonse;ndidzayimba nyimbo zokutamandani pamaso pa “milungu.”

2Ndidzagwada kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyerandipo ndidzayamika dzina lanuchifukwa cha chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu,pakuti Inu mwakuza dzina lanu ndi mawu anukupambana zinthu zonse.

3Pamene ndinayitana, munandiyankha;munandisandutsa wamphamvu ndi wolimba mtima.

4Mafumu onse a dziko lapansi akuyamikeni Yehova,pamene amva mawu a pakamwa panu.

5Iwo ayimbe za njira za Yehova,pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.

6Ngakhale kuti Yehova ngokwezeka, amasamalira odzichepetsa,koma anthu onyada amawadziwira chapatali.

7Ngakhale ndiyende pakati pa masautso,mumasunga moyo wanga;mumatambasula dzanja lanu kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga,mumandipulumutsa ndi dzanja lanu lamanja.

8Yehova adzakwaniritsa cholinga chake pa ine;chikondi chanu chosasinthika Yehova, ndi chosathamusasiye ntchito ya manja anu.

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]