Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 15 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Za Kulangidwa kwa Mowabu

1Uthenga wonena za Mowabu:Popeza kuti mu usiku umodzi wokha mzinda wa Ari wa ku Mowabu wawonongedwa,wawonongedwa pa usiku umodzi wokha.Mzinda wa Kiri wawonongedwa,wawonongedwa pa usiku umodzi wokha.

2Anthu a ku Diboni akupita ku nyumba ya milungu yawo,akupita ku malo awo achipembedzo kukalira;anthu a ku Mowabu akulirira mofuwula mzinda wa Nebo ndi wa Medeba.Mutu uliwonse wametedwa mpala,ndipo ndevu zonse zametedwa.

3Mʼmisewu akuvala ziguduli;pa madenga ndi mʼmabwaloaliyense akulira mofuwula,misozi ili pupupu.

4Anthu a ku Hesiboni ndi Eleali akulira mofuwula,mawu awo akumveka mpaka ku Yahazi.Kotero asilikali a ku Mowabu akulira mofuwula,ndipo ataya mtima.

5Inenso ndikulirira Mowabu;chifukwa othawa nkhondo ake akupita akulira ku chikweza cha Luluti mpaka ku Zowarindi Egilati-Selisiyaakupita akulira ku chikweza cha Luhiti,Akulira mosweka mtimapa njira yopita ku Horonaimu;akulira mosweka mtima chifukwa cha chiwonongeko chawo.

6Madzi a ku Nimurimu aphwandipo udzu wauma;zomera zawonongekandipo palibe chomera chobiriwira chatsala.

7Kotero kuti chuma chomwe anachipeza ndi kuchisunga,achitenga kuti awoloke nacho chigwembe cha Misondozi.

8Kulira kwawo kukumveka mʼdziko lonse la Mowabu;kulira kwawo kosweka mtima kukumvekampaka ku Egilaimu ndi Beeri-Elimu.

9Madzi a ku Dimoni afiira ndi magazi,komabe ndidzabweretsa zina zambiri pa Dimoni,mkango woti udzagwire aliyense othawa mu Mowabundi aliyense wotsala mʼdzikomo.

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]