Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Jeremiah 47 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Uthenga Wonena za Afilisti

1Uthenga umene Yehova anamupatsa mneneri Yeremiya wonena za Afilisti, Farao asanathire nkhondo Gaza ndi uwu:

2Yehova akuti,“Taonani mmene madzi akubwerera kuchokera kumpoto;adzasanduka mtsinje wosefukira ndi a mkokomo.Adzasefukira mʼdziko monse ndi kumiza chilichonse mʼmenemo,mizinda ndi onse okhala mʼmenemo.Anthu adzafuwula;anthu onse okhala mʼdzikomo adzalira

3akadzamva mgugu wa ngʼombe zazimuna zothamanga,phokoso la magaleta akendi kulira kwa mikombero yake.Makolo sadzatembenuka kuti athandize ana awo;manja awo adzangoti khoba.

4Pakuti tsiku lafikalowononga Afilisti onsendi kupha onse otsala,onse amene akanatha kuthandiza Turo ndi Sidoni.Yehova ali pafupi kuwononga Afilisti,otsala ochokera ku zilumba za ku Kafitori.

5Anthu a ku Gaza ameta mipala;anthu a ku Asikeloni akhala chete.Inu otsala a ku chigwa,mudzakhala mukudzichekacheka mpaka liti?

6“Mukulira kuti, ‘Aa, lupanga la Yehova,kodi udzapumula liti?Bwerera mʼmalo ako;ukhale momwemo ndipo ukhale chete.’

7Koma lupangalo lidzapumula bwanjipamene Yehova walilamulirakuti lithire nkhondoAsikeloni ndi anthu a mʼmbali mwa nyanja?”

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]