Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Psalms 146 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

1Tamandani Yehova.Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.

2Ndidzatamanda Yehova ndi moyo wanga wonse;ndidzayimba nyimbo zamatamando kwa Mulungu wanga nthawi yonse ya moyo wanga.

3Musamadalire mafumu,anthu osakhalitsa, amene sangathe kupulumutsa.

4Pamene mizimu yawo yachoka, iwo amabwerera ku dothi;zimene ankafuna kuchita zimatha tsiku lomwelo.

5Wodala ndi amene thandizo lake ndiMulungu wa Yakobo.

6Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi,nyanja ndi zonse zili mʼmenemo;Yehova, amene ndi wokhulupirika kwamuyaya.

7Iye amachitira chilungamo anthu oponderezedwandipo amapereka chakudya kwa anthu anjala.Yehova amamasula amʼndende,

8Yehova amatsekula maso anthu osaona,Yehova amadzutsa onse amene awerama pansi,Yehova amakonda anthu olungama.

9Yehova amasamalira alendondipo amathandiza ana ndi akazi amasiye,koma amasokoneza njira za anthu oyipa.

10Yehova ndiye Mfumu mpaka muyaya,Mulungu wako iwe Ziyoni, pa mibado yonse.Tamandani Yehova.

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]