Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Psalms 145 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Salimo la matamando la Davide.

1Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu yanga;ndidzatamanda dzina lanu ku nthawi za nthawi.

2Ndidzakutamandani tsiku ndi tsikundi kulemekeza dzina lanu ku nthawi za nthawi.

3Yehova ndi wamkulu ndi woyenera matamando onse;ukulu wake palibe angawumvetsetse.

4Mʼbado wina udzayamikira ntchito yanu kwa mʼbado wina;Iwo adzafotokoza za machitidwe anu amphamvu.

5Adzayankhula ulemerero wokongola waufumu wanu,ndipo ine ndidzalingalira za ntchito zanu zodabwitsa.

6Iwo adzafotokoza za mphamvu ya ntchito zanu zoopsa kwambiri,ndipo ine ndidzalengeza za ntchito zanu zazikulu.

7Adzakondwerera kuchuluka kwa ubwino wanu,ndi kuyimba mwachimwemwe za chilungamo chanu.

8Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo,wosakwiya msanga ndi wodzaza ndi chikondi chosasinthika.

9Yehova ndi wabwino kwa onse;amachitira chifundo zonse zimene anazipanga.

10Zonse zimene munazipanga zidzakutamandani, Inu Yehova;oyera mtima adzakulemekezani.

11Iwo adzafotokoza za ulemerero wa ufumu wanundi kuyankhula za mphamvu yanu,

12kuti anthu onse adziwe za machitidwe anu amphamvundi ulemerero wokongola wa ufumu wanu.

13Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya,ndipo ulamuliro wanu ndi wosatha pa mibado yonse.Yehova ndi wokhulupirika pa malonjezo ake onsendi wokonda zonse zimene Iye anazipanga.

14Yehova amagwiriziza onse amene akugwandipo amakweza onse otsitsidwa.

15Maso a onse amayangʼana kwa Inu,ndipo Inu mumawapatsa chakudya chawo pa nthawi yoyenera.

16Mumatsekula dzanja lanundi kukwaniritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.

17Yehova ndi wolungama mʼnjira zake zonse,ndi wokonda zonse zimene anazipanga.

18Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuyitana,onse amene amamuyitana Iye mʼchoonadi.

19Iye amakwaniritsa zokhumba za iwo amene amamuopa;amamva kulira kwawo ndi kuwapulumutsa.

20Yehova amayangʼana onse amene amamukondakoma adzawononga anthu onse oyipa.

21Pakamwa panga padzayankhula zotamanda Yehova.Cholengedwa chilichonse chitamande dzina lake loyeraku nthawi za nthawi.

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]