Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Ecclesiastes 11 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Cast your bread upon the waters, for after many days you will find it again. Ponya chakudya chako pa madzi, udzachipezanso patapita masiku ambiri.
2 Give a portion to seven, or even to eight, for you do not know what disaster may come upon the land. Ndalama zako uzisungitse kwa anthu asanu ndi awiri, inde kwa anthu asanu ndi atatu, pakuti sudziwa ndi tsoka lanji limene likubwera pa dziko.
3 If the clouds are full, they pour out rain upon the earth; and if a tree falls to the south or to the north, in the place where it falls, there it will lie. Ngati mitambo yadzaza ndi madzi, imagwetsa mvula pa dziko lapansi. Mtengo ukagwera cha kummwera kapena cha kumpoto, ndiye kuti udzagonera kumene wagwerako.
4 Whoever watches the wind will never sow, and whoever studies the clouds will never reap. Amene amayangʼana mphepo sadzadzala; amene amayangʼana mitambo sadzakolola.
5 Just as you do not know the path of the wind, or how the bones are formed in the womb of a pregnant woman, so you cannot know the work of God, who makes everything. Momwe sudziwira mayendedwe a mphepo, kapena momwe mzimu umalowera mʼthupi la mwana mʼmimba mwa amayi, momwemonso sungathe kudziwa ntchito za Mulungu, Mlengi wa zinthu zonse.
6 Sow your seed in the morning, and at evening do not let your hand rest, for you do not know which will succeed—this or that—or whether both alike will do well. Dzala mbewu zako mmawa ndipo madzulo usamangoti manja lobodo, pakuti sudziwa chimene chidzapindula, mwina ichi kapena icho, kapena mwina zonse ziwiri zidzachita bwino.
7 Light is sweet, and it is pleasant for the eyes to see the sun. Kuwala nʼkwabwino, ndipo maso amasangalala kuona dzuwa.
8 So if a person lives many years, let them rejoice in them all; but let them remember the days of darkness, for they will be many. Everything that comes is fleeting. Munthu akakhala wa zaka zambiri, mulekeni akondwerere zaka zonsezo, koma iye azikumbukira masiku a mdima, pakuti adzakhala ochuluka. Chilichonse chimene chikubwera ndi chopanda phindu.
9 Rejoice, young man, in your youth, and let your heart give you gladness in the days of your youth. Walk in the ways of your heart and in the sight of your eyes; but know that for all these things God will bring you into judgment. Kondwera mnyamata iwe, pamene ukanali wamngʼono, ndipo mtima wako usangalale pa nthawi ya unyamata wako. Tsatira zimene mtima wako ukufuna, ndiponso zimene maso ako akuona, koma dziwa kuti pa zinthu zonsezo Mulungu adzakuweruza.
10 So banish frustration from your heart, and put away pain from your body, for youth and the dawn of life are fleeting. Choncho uchotse zokusautsa mu mtima mwako, upewe zokupweteka mʼthupi mwako, pakuti unyamata ndi ubwana ndi zopandapake.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]