Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Ecclesiastes 10 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Dead flies make the perfumer's oil stink and ferment; so a little foolishness outweighs wisdom and honor. Monga ntchentche zakufa zimayika fungo loyipa mʼmafuta onunkhira, choncho kupusa pangʼono kumawononganso nzeru ndi ulemu.
2 The heart of the wise inclines to his right, but the heart of a fool to his left. Mtima wa munthu wanzeru umamutsogolera bwino, koma mtima wa munthu wopusa umamusocheretsa.
3 Even when the fool walks along the road, he lacks sense, and he shows everyone that he is a fool. Chitsiru ngakhale chikamayenda mu msewu, zochita zake ndi zopanda nzeru ndipo chimaonetsa aliyense kuti icho ndi chitsirudi.
4 If the ruler's anger rises against you, do not leave your post, for calmness lays great offenses to rest. Ngati wolamulira akukwiyira, usachoke pa ntchito yako; kufatsa kumakonza zolakwa zazikulu.
5 There is an evil I have seen under the sun, the kind of error that comes from a ruler: Pali choyipa chimene ndinachiona pansi pano, kulakwitsa kumene kumachokera kwa wolamulira:
6 foolishness is set in many high places, while the rich sit in low positions. Zitsiru amazipatsa ntchito zambiri zapamwamba, pamene anthu olemera amawapatsa ntchito zotsika.
7 I have seen slaves on horseback, and princes walking on foot like slaves. Ndaona akapolo atakwera pa akavalo, pamene akalonga akuyenda pansi ngati akapolo.
8 Whoever digs a pit may fall into it, and whoever breaks through a wall may be bitten by a snake. Amene amakumba dzenje adzagwamo yekha; amene amabowola khoma adzalumidwa ndi njoka.
9 Whoever quarries stones may be hurt by them, and whoever splits logs is endangered by them. Amene amaphwanya miyala adzapwetekedwa ndi miyalayo; amene amawaza nkhuni adzapwetekedwa nazo.
10 If the axe is dull and its edge is not sharpened, you have to use more strength; but wisdom brings success. Ngati nkhwangwa ili yobuntha yosanoledwa, pamafunika mphamvu zambiri potema, koma luso limabweretsa chipambano.
11 If the snake bites before it is charmed, the charmer gains nothing. Nʼkopanda phindu kudziwa kuseweretsa njoka ngati njokayo yakuluma kale.
12 A wise man's words bring him favor, but the lips of a fool consume him. Mawu a pakamwa pa munthu wanzeru ndi okondweretsa, koma chitsiru chidzawonongedwa ndi milomo yake yomwe.
13 The beginning of his words is foolishness, and the end of his talk is wicked madness. Chitsiru chimayamba ndi mawu opusa; potsiriza pake zoyankhula zake ndi zamisala
14 Yet the fool keeps on talking. No one knows what is coming, and who can tell anyone what will happen after him? ndipo chitsiru chimachulukitsa mawu. Palibe amene amadziwa zimene zikubwera mʼtsogolo, ndani angamuwuze zomwe zidzachitika iye akadzafa?
15 Fools wear themselves out with their work, for they do not even know the way to town. Chitsiru chimatopa msanga ndi ntchito yochepa; ndipo sichikhala ndi mphamvu zobwererera ku mudzi.
16 Woe to you, land, when your king is a child and your princes feast in the morning. Tsoka kwa iwe, iwe dziko ngati mfumu yako ikali mwana, ndipo atsogoleri ako amakhala pa madyerero mmamawa.
17 Blessed are you, land, when your king is the son of nobles and your princes feast at the proper time—for strength, and not for drunkenness. Wodala iwe, iwe dziko ngati mfumu yako ndi mwana wolemekezeka ndipo atsogoleri ako amadya pa nthawi yake, kuti apeze mphamvu osati kuti aledzere.
18 Through laziness the rafters sag, and through idle hands the house leaks. Ngati munthu ndi waulesi, denga lake limaloshoka; ngati manja ake ndi alobodo nyumba yake imadontha.
19 Bread is made for laughter, and wine gladdens life, and money answers everything. Phwando ndi lokondweretsa anthu, ndipo vinyo ndi wosangalatsa moyo, koma ndalama ndi yankho la chilichonse.
20 Do not curse the king even in your thoughts, and do not curse the rich even in your bedroom, for a bird of the sky may carry your words, and a winged creature may report what you say. Usanyoze mfumu ngakhale mu mtima mwako, kapena kutukwana munthu wachuma mʼchipinda chako, pakuti mbalame yamlengalenga itha kutenga mawu ako nʼkukafotokoza zomwe wanena.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]