Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Psalms 19 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

1Zakumwamba zimalengeza za ulemerero wa Mulungu;thambo limalalikira ntchito za manja ake.

2Tsiku ndi tsiku zimayankhula mawu ambiri,usiku ndi usiku zimaonetsa poyera nzeru.

3Palibe kuyankhula, palibe mawu aliwonse;liwu lawo silimveka.

4Koma uthenga wawo umapita pa dziko lonse lapansi,mawuwo amafika mpakakumalekezero a dziko lapansi.

5Dzuwa lili ngati mkwatibwi wobwera kuchokera ku nsanja yake,ngati katswiri wokondwerera kuthamanga pa mpikisano.

6Limatuluka kuyambira mbali ina ya thambondi kuzungulira mpaka mbali inanso;palibe chinthu chotha kupewa kutentha kwake.

7Lamulo la Yehova ndi langwiro,kutsitsimutsa moyo.Maumboni a Yehova ndi odalirika,amapereka nzeru kwa wopanda nzeru.

8Malangizo a Yehova ndi olungama,amapereka chimwemwe mu mtima.Malamulo a Yehova ndi onyezimira,amapereka kuwala.

9Kuopa Yehova ndiye chinthu changwiro,chimakhala mpaka muyaya.Maweruzo a Yehova ndi owonandipo onse ndi olungama;

10ndi a mtengowapatali kuposa golide,kuposa golide weniweni;ndi otsekemera kuposa uchi,kuposa uchi wochokera pa chisa chake.

11Mtumiki wanu amachenjezedwa nawo;powasunga pali mphotho yayikulu.

12Ndani angathe kudziwa zolakwa zake?Mundikhululukire zolakwa zanga zobisika.

13Muteteze mtumiki wanunso ku machimo ochita akudziwa;iwo asandilamulire.Kotero ndidzakhala wosalakwa,wopanda mlandu wa tchimo lalikulu.

14Mawu a mʼkamwa mwanga ndi zolingalira za mu mtima mwangazikhale zokondweretsa pamaso panu,Inu Yehova, Thanthwe langa ndi Mpulumutsi wanga.

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]