Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 18 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Whoever isolates himself pursues his own desire; he lashes out against all sound wisdom. Munthu wokonda kukhala yekha amafunafuna zomukomera yekha; iye amatsutsana ndi malangizo onse anzeru.
2 A fool takes no pleasure in understanding, but only in airing his own opinions. Chitsiru chilibe chidwi chomvetsa zinthu, koma chimakondwera ndi kuyankhula maganizo ake okha.
3 When wickedness comes, contempt comes too, and with dishonor comes reproach. Kuyipa mtima kukabwera, manyozonso amabwera. Manyazi amabwera pamodzi ndi kunyozeka.
4 The words of a person's mouth are deep waters; the fountain of wisdom is a flowing stream. Mawu a munthu ali ngati madzi akuya, kasupe wa nzeru ndiye mtsinje wotumphuka.
5 It is not good to show partiality to the wicked, denying justice to the righteous. Si kwabwino kukondera munthu woyipa pa milandu; kapena kupondereza munthu wosalakwa.
6 A fool's lips bring strife, and his mouth invites a beating. Mawu a chitsiru amautsa mkangano; pakamwa pake pamayitana mkwapulo.
7 A fool's mouth is his ruin, and his lips are a snare to his soul. Pakamwa pa chitsiru ndipo pamabweretsa chiwonongeko chake, ndipo milomo yake ili ngati msampha wa moyo wake.
8 The words of a gossip are like choice morsels; they go down into the inmost being. Mawu a miseche ali ngati chakudya chokoma; amalowa mʼmimba mwa munthu.
9 Whoever is slack in his work is brother to one who destroys. Munthu waulesi pa ntchito yake ali pachibale ndi munthu amene amawononga zinthu.
10 The name of our Father is a strong tower; the righteous runs into it and is safe. Dzina la Yehova lili ngati nsanja yolimba; wolungama amathawiramo napulumuka.
11 A rich man's wealth is his fortified city; in his imagination it is like a high wall. Chuma cha anthu olemera chili ngati mzinda wake wolimba; chili ngati khoma lalitali limene amaganiza kuti limutchinjiriza.
12 Before destruction the human heart is proud, but humility comes before honor. Chiwonongeko chisanafike, mtima wa munthu umakhala wonyada, koma ulemu umatsatira kudzichepetsa.
13 If one answers before he listens, it is his foolishness and his shame. Ukayankha usanamvetse bwino nkhani, umenewo ndi uchitsiru ndipo umachita manyazi.
14 A person's spirit can sustain him through sickness, but a crushed spirit—who can bear it? Mtima wa munthu utha kupirira pa matenda, koma munthu akataya mtima ndani angathe kumulimbitsanso.
15 The discerning heart acquires knowledge, and the ear of the wise seeks it out. Munthu wanzeru amawonjezera nzeru zina; amafunafuna kudziwa bwino zinthu.
16 A person's gift opens the way for him and brings him before important people. Mphatso ya munthu imamutsekulira njira yomufikitsa pamaso pa anthu akuluakulu.
17 The first to state his case seems right, until another comes and examines him. Amene amayamba kufotokoza mlandu wake amaoneka ngati wolungama ndiye mpaka mnzake atabwera ndi kumufunsa bwino.
18 Casting the lot settles disputes and separates strong opponents. Kuchita maere kumathetsa mikangano; amalekanitsa okangana amphamvu.
19 An offended brother is harder to win than a fortified city, and disputes are like the bars of a fortress. Mʼbale amene wamuthandiza amakhala ngati mzinda wolimba, koma kukangana naye kumatsekereza thandizo.
20 From the fruit of a person's mouth his stomach is satisfied; with the yield of his lips he is filled. Munthu amapeza bwino malingana ndi zoyankhula zake. Adzakhuta ndi zipatso za pakamwa pake.
21 Death and life are in the power of the tongue, and those who love it will eat its fruit. Mawu ako angathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo. Wokonda kuyankhulayankhula adzadya zipatso zake.
22 He who finds a wife finds what is good and receives favor from our Father. Wapeza mkazi wapeza chinthu chabwino ndipo Yehova amamukomera mtima.
23 The poor person pleads for mercy, but the rich answers harshly. Munthu wosauka amapempha koma munthu wolemera amayankha mwaukali.
24 A man of many companions may come to ruin, but there is a friend who sticks closer than a brother. Pali abwenzi amene chibwenzi chawo nʼchapamaso, koma pali bwenzi limene limakukangamira kuposa mʼbale wako.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]