Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 17 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Better a dry crust eaten in peace than a house full of feasting with strife. Nʼkwabwino kudya mkute koma pali mtendere, kuposa kuchita madyerero mʼnyumba mʼmene muli mikangano.
2 A prudent servant will rule over a disgraceful son and will share the inheritance among the brothers. Kapolo wanzeru adzalamulira mwana wochititsa manyazi, ndipo kapoloyo adzagawana nawo cholowa ngati mmodzi mwa abale.
3 The crucible is for silver and the furnace for gold, but our Father tests hearts. Siliva amamuyesa mʼngʼanjo ndipo golide amamuyesa mʼngʼanjo, koma Yehova amayesa mitima.
4 An evildoer listens to wicked lips; a liar listens to a destructive tongue. Munthu woyipa amamvera malangizo oyipa; munthu wabodza amatchera khutu mawu osakaza.
5 Whoever mocks the poor insults his Maker; whoever gloats over disaster will not go unpunished. Iye amene amalalatira mʼmphawi amanyoza mlengi wake; amene amakondwerera tsoka la mnzake sadzakhala osalangidwa.
6 Grandchildren are the crown of the aged, and the glory of children is their parents. Zidzukulu ndiye ulemu wa anthu okalamba, ndipo makolo ndiye ulemerero wa ana.
7 Fine speech is not fitting for a fool—still less are lying lips for a noble. Kuyankhula bwino sikuyenerana ndi chitsiru, nanji kuyankhula bodza kungayenerane kodi ndi mfumu?
8 A bribe seems like a magic charm to the one who gives it; wherever he turns, he thinks he will succeed. Chiphuphu chili ngati mankhwala amwayi kwa wochiperekayo; kulikonse kumene amapita zinthu zimamuyendera.
9 Whoever covers an offense seeks love, but whoever keeps bringing it up separates close friends. Iye amene amakhululukira zolakwa za wina, amafunitsitsa chikondi; wobwerezabwereza nkhani amapha chibwenzi.
10 A rebuke goes deeper into a person of understanding than one hundred blows into a fool. Munthu wanzeru amamva kamodzi kokha, munthu wopanda nzeru ndi samvamkunkhu.
11 A rebellious man seeks only evil, and a cruel messenger will be sent against him. Munthu woyipa maganizo ake ali pa kuwukira basi; ndipo bwana adzamutumizira wamthenga wankhanza.
12 Better to meet a bear robbed of her cubs than a fool in his foolishness. Nʼkwabwino kukumana ndi chimbalangondo cholandidwa ana ake kusiyana ndi kukumana ndi chitsiru mu uchitsiru wake.
13 If anyone returns evil for good, evil will never leave his house. Ngati munthu abwezera choyipa kusinthana ndi zabwino, ndiye choyipa sichidzachoka mʼnyumba mwake.
14 Starting a quarrel is like breaching a dam, so drop the dispute before it bursts out. Chiyambi cha mikangano chili ngati kukhamulira madzi, choncho uzichokapo mkangano usanayambe.
15 Whoever justifies the wicked and whoever condemns the righteous—both alike are detestable to our Father. Kumasula munthu wolakwa kapena kumanga munthu wosalakwa, zonse ziwirizi Yehova zimamunyansa.
16 Why should a fool have money in hand to buy wisdom, when he has no heart to learn? Ndalama zogulira nzeru zili ndi phindu lanji mʼmanja mwa chitsiru poti iyeyo mutu wake sumayenda bwino?
17 A friend loves at all times, and a brother is born for a time of trouble. Bwenzi lako limakukonda nthawi zonse, ndipo mʼbale wako anabadwa kuti azikuthandiza pamavuto.
18 One who lacks sense shakes hands on a pledge and puts up security for his neighbor. Munthu wopanda nzeru amavomereza zopereka chikole ndipo iyeyo amasanduka chikole cha mnansi wake.
19 Whoever loves wrongdoing loves strife; whoever builds his gate high invites destruction. Wokonda zolakwa amakonda mkangano, ndipo wokonda kuyankhula zonyada amadziyitanira chiwonongeko.
20 A crooked heart finds no good, and a twisted tongue falls into trouble. Munthu wamtima woyipa zinthu sizimuyendera bwino; ndipo woyankhula zachinyengo amagwa mʼmavuto.
21 Whoever fathers a fool brings grief on himself; the father of a godless fool has no joy. Mwana wopusa amamvetsa chisoni abambo ake, abambo a chitsiru sakhala ndi chimwemwe.
22 A joyful heart is good medicine, but a crushed spirit dries up the bones. Mtima wosangalala uli ngati mankhwala abwino, koma mtima wokhumudwa umafowoketsa mafupa.
23 A wicked man takes a bribe in secret to pervert the ways of justice. Munthu woyipa amalandira chiphuphu chamseri kuti apotoze chiweruzo cholungama.
24 A discerning person keeps wisdom in view, but the eyes of a fool wander to the ends of the earth. Munthu wozindikira zinthu, maso ake amakhala pa nzeru, koma chitsiru chimwazamwaza maso ake pa dziko lonse lapansi.
25 A foolish son is a grief to his father and bitterness to the mother who bore him. Mwana wopusa amamvetsa chisoni abambo ake ndipo amapweteketsa mtima amayi ake.
26 To punish the righteous is not good, nor to flog the noble for their integrity. Sibwino kulipitsa munthu wosalakwa, kapena kulanga anthu osalakwa.
27 Whoever holds back his words has knowledge, and one with a calm spirit is a person of understanding. Munthu wosunga pakamwa ndiye wodziwa zinthu, ndipo wodekha mtima ndiye womvetsa bwino zinthu.
28 Even a fool who keeps silent is thought wise; when he closes his lips, he seems discerning. Ngakhale chitsiru chimakhala ngati chanzeru chikakhala chete; ndipo chikatseka pakamwa chimakhala ngati munthu wochenjera.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]