Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 16 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 The plans of the heart belong to man, but the answer of the tongue comes from our Father. Zolinga za mu mtima ndi za munthu, koma kwa Yehova ndiye kumachokera yankho.
2 All a man's ways are pure in his own eyes, but our Father weighs the motives. Zochita zonse za munthu zimaoneka zabwino pamaso pake, koma Yehova ndiye amasanthula zolinga zako.
3 Commit your works to our Father, and your plans will be established. Pereka ntchito zako zonse mʼmanja mwa Yehova, ndipo zolinga zako zidzachitikadi.
4 Our Father has made everything for its purpose, even the wicked for the day of trouble. Yehova amachita zonse ndi cholinga chake, ngakhale anthu oyipa kuti aone tsiku latsoka.
5 Everyone proud of heart is detestable to our Father; be assured, he will not go unpunished. Munthu aliyense wodzikuza amamunyansa Yehova. Koma dziwani izi: Iwo sadzakhala osalangidwa.
6 Loving devotion and faithfulness atone for sin, and the fear of our Father turns a person away from evil. Chifukwa cha chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika, munthu amakhululukidwa machimo ake; chifukwa cha kuopa Yehova munthu amapewa zoyipa.
7 When a man's ways please our Father, our Father makes even the man's enemies live at peace with him. Pamene makhalidwe a munthu akondweretsa Yehova, ngakhale adani ake amakhala naye mwa mtendere.
8 Better a little with righteousness than great income with injustice. Kuli bwino kukhala ndi zinthu pangʼono zozipeza mwachilungamo, kusiyana ndi kukhala ndi zinthu zambiri zozipeza popanda chilungamo.
9 The heart of man plans his way, but our Father establishes his steps. Mtima wa munthu umalingalira zochita, koma Yehova ndiye amakhazikitsa njira zake.
10 A divine verdict is on the lips of a king; his mouth does not betray justice. Mawu a mfumu ali ngati mawu ochokera kwa Mulungu; ndipo pakamwa pake sipalakwa poweruza mlandu.
11 Honest scales and balances belong to our Father; every weight and measure is his work. Miyeso ndi masikelo achilungamo zimachokera kwa Yehova; miyala yonse yoyesera ya mʼthumba anayipanga ndi Yehova.
12 It is detestable for kings to do wickedness, for a throne is established through righteousness. Kuchita zoyipa kumanyansa mafumu, pakuti chilungamo ndiye maziko a ufumu wake.
13 Righteous lips are the delight of kings, and they love the one who speaks what is right. Mawu owona amakondweretsa mfumu. Iyo imakonda munthu woyankhula choonadi.
14 A king's wrath is a messenger of death, but a wise man will appease it. Ukali wa mfumu ndi mthenga wa imfa, koma munthu wanzeru amawupepesa ukaliwo.
15 In the light of a king's face is life, and his favor is like a cloud bringing the spring rain. Kuwala kwa nkhope ya mfumu kumapatsa moyo; ndipo kukoma mtima kwake kuli ngati mitambo ya mvula nthawi ya chilimwe.
16 How much better to get wisdom than gold! Getting understanding is worth more than silver. Nʼkwabwino kwambiri kupeza nzeru kupambana golide. Kukhala womvetsa bwino zinthu nʼkwabwino kupambana ndi kukhala ndi siliva.
17 The highway of the upright turns away from evil; whoever guards his way protects his life. Msewu wa munthu wowongoka mtima umapewa zoyipa; wopenyetsetsa kumene akupita amasunga moyo wake.
18 Pride goes before destruction, and a haughty spirit before a fall. Kunyada kumafikitsa ku chiwonongeko, ndipo munthu wodzikuza adzagwa.
19 Better to be lowly in spirit among the poor than to share the plunder with the proud. Nʼkwabwino kukhala ndi mtima wodzichepetsa pakati pa anthu oponderezedwa, kusiyana ndi kugawana zolanda ndi anthu onyada.
20 Whoever heeds the word will find good, and blessed is the one who trusts in our Father. Munthu womvera malangizo zinthu zimamuyendera bwino, ndipo wodala ndi amene amadalira Yehova.
21 The wise of heart is called discerning, and pleasant speech increases persuasiveness. A mtima wanzeru amatchedwa ozindikira zinthu, ndipo mawu ake okoma amawonjezera nzeru.
22 Understanding is a fountain of life to the one who has it, but fools are corrected by their own foolishness. Kumvetsa zinthu ndi kasupe wa moyo kwa iwo amene ali nako, koma uchitsiru umabweretsa chilango kwa zitsiru.
23 The heart of the wise makes his speech wise and adds persuasiveness to his lips. Mtima wanzeru umathandiza munthu kuyankhula mwa nzeru, ndipo mawu ake amawonjezera nzeru.
24 Pleasant words are a honeycomb, sweet to the soul and healing to the bones. Mawu okometsera ali ngati chisa cha njuchi, amakoma mu mtima ndipo amalimbitsa thupi.
25 There is a way that seems right to a man, but its end is the way of death. Pali njira ina yooneka ngati yowongoka kwa munthu koma kumatsiriziro kwake ndi imfa.
26 A worker's appetite works for him; his hunger drives him on. Njala ya munthu wantchito imamuthandiza kulimbikira; njalayo imamukakamiza kuchitapo kanthu.
27 A worthless man digs up evil, and on his lips is a scorching fire. Munthu wopanda pake amakonzekera kuchita zoyipa ndipo mawu ake ali ngati moto wopsereza.
28 A perverse man spreads strife, and a gossip separates close friends. Munthu woyipa mtima amayambitsa mikangano, ndipo miseche imalekanitsa anthu okondana kwambiri.
29 A violent man entices his neighbor and leads him down a harmful path. Munthu wandewu amakopa mnansi wake, ndipo amamuyendetsa njira imene si yabwino.
30 Whoever winks his eyes plots perversity; whoever purses his lips is bent on evil. Amene amatsinzinira maso ake amalingalira zinthu zokhota; amene amachita msunamo amakonzeka kuchita zoyipa.
31 Gray hair is a crown of glory; it is gained in the way of righteousness. Imvi zili ngati chipewa chaufumu chaulemerero; munthu amazipeza akakhala moyo wolungama.
32 Better a patient person than a mighty one, and one who rules his spirit than one who takes a city. Munthu wosapsa mtima msanga amaposa munthu wankhondo, munthu wowugwira mtima wake amaposa amene amalanda mzinda.
33 The lot is cast into the lap, but its every decision is from our Father. Maere amaponyedwa pa mfunga, koma ndiye Yehova amene amalongosola zonse.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]