Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 15 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 A gentle answer turns away wrath, but a harsh word stirs up anger. Kuyankha kofatsa kumathetsa mkwiyo, koma mawu ozaza amautsa ukali.
2 The tongue of the wise commends knowledge, but the mouths of fools pour out foolishness. Munthu wanzeru amayankhula zinthu za nzeru, koma pakamwa pa zitsiru pamatulutsa za uchitsiru.
3 The eyes of our Father are in every place, keeping watch on the evil and the good. Maso a Yehova ali ponseponse, amayangʼana pa oyipa ndi abwino omwe.
4 A gentle tongue is a tree of life, but a corrupt tongue crushes the spirit. Kuyankhula kodekha kuli ngati mtengo wopatsa moyo, koma kuyankhula kopotoka kumapweteka mtima.
5 A fool despises his father's instruction, but whoever heeds correction is prudent. Chitsiru chimanyoza mwambo wa abambo ake, koma wochenjera amasamala chidzudzulo.
6 In the house of the righteous there is much treasure, but the income of the wicked brings trouble. Munthu wolungama amakhala ndi chuma chambiri, zimene woyipa amapindula nazo zimamugwetsa mʼmavuto.
7 The lips of the wise spread knowledge, but not so the hearts of fools. Pakamwa pa anthu anzeru pamafalitsa nzeru; koma mitima ya zitsiru sitero.
8 The sacrifice of the wicked is detestable to our Father, but the prayer of the upright is his delight. Nsembe za anthu oyipa zimamunyansa Yehova, koma amakondwera ndi pemphero la anthu owona mtima.
9 The way of the wicked is detestable to our Father, but he loves the one who pursues righteousness. Ntchito za anthu oyipa zimamunyansa Yehova koma amakonda amene amafunafuna chilungamo.
10 There is severe discipline for the one who leaves the path, and whoever hates correction will die. Amene amasiya njira yabwino adzalangidwa koopsa. Odana ndi chidzudzulo adzafa.
11 The grave and Destruction lie open before our Father; how much more the hearts of all people! Manda ndi chiwonongeko ndi zosabisika pamaso pa Yehova, nanji mitima ya anthu!
12 A scoffer does not love to be corrected; he will not go to the wise. Wonyoza sakonda kudzudzulidwa; iye sapita kwa anthu anzeru.
13 A glad heart makes a cheerful face, but a sorrowful heart crushes the spirit. Mtima wokondwa umachititsa nkhope kukhala yachimwemwe, koma mtima wosweka umawawitsa moyo.
14 A discerning heart seeks knowledge, but the mouths of fools feed on foolishness. Mtima wa munthu wozindikira zinthu umafunafuna nzeru, koma pakamwa pa zitsiru pamadya uchitsiru wawo.
15 All the days of the afflicted are hard, but a cheerful heart has a continual feast. Munthu woponderezedwa masiku ake onse amakhala oyipa, koma mtima wachimwemwe umakhala pa chisangalalo nthawi zonse.
16 Better a little with the fear of our Father than great treasure and trouble with it. Kuli bwino kukhala ndi zinthu pangʼono nʼkumaopa Yehova, kusiyana ndi kukhala ndi chuma chambiri uli pamavuto.
17 Better a meal of vegetables where there is love than a fattened ox with hatred. Kuli bwino kudyera ndiwo zamasamba pamene pali chikondi, kusiyana ndi kudyera nyama yangʼombe yonenepa pamene pali udani.
18 A hot-tempered man stirs up strife, but one who is slow to anger calms a quarrel. Munthu wopsa mtima msanga amayambitsa mikangano, koma munthu woleza mtima amathetsa ndewu.
19 The way of the lazy is like a hedge of thorns, but the path of the upright is a level highway. Njira ya munthu waulesi ndi yowirira ndi mtengo waminga, koma njira ya munthu wolungama ili ngati msewu waukulu.
20 A wise son makes a glad father, but a foolish man despises his mother. Mwana wanzeru amakondweretsa abambo ake, koma mwana wopusa amanyoza amayi ake.
21 Foolishness is joy to one who lacks sense, but a person of understanding walks a straight path. Uchitsiru umakondweretsa munthu wopanda nzeru, koma munthu womvetsa zinthu amayenda mowongoka.
22 Plans fail without counsel, but with many advisers they succeed. Popanda uphungu zolinga zako munthu zimalephereka, koma pakakhala aphungu ambiri zolinga zimatheka.
23 A person finds joy in giving an apt reply, and how good is a word at the right time! Munthu amakondwera ndi kuyankha koyenera, ndipo mawu onena pa nthawi yake ndi okoma.
24 The path of life leads upward for the prudent, turning him away from the grave below. Munthu wanzeru amatsata njira yopita ku moyo kuti apewe malo okhala anthu akufa.
25 Our Father tears down the house of the proud, but he protects the widow's boundary. Yehova amapasula nyumba ya munthu wonyada koma amasamalira malo a mkazi wamasiye.
26 The thoughts of the wicked are detestable to our Father, but gracious words are pure. Maganizo a anthu oyipa amamunyansa Yehova, koma mawu a anthu oyera mtima amamusangalatsa.
27 Whoever is greedy for unjust gain brings trouble on his own household, but the one who hates bribes will live. Munthu wofuna phindu mwachinyengo amavutitsa banja lake, koma wodana ndi ziphuphu adzakhala ndi moyo.
28 The heart of the righteous weighs how to answer, but the mouth of the wicked pours out evil. Munthu wolungama amaganizira za mmene ayankhire, koma pakamwa pa munthu woyipa pamatulutsa mawu oyipa.
29 Our Father is far from the wicked, but he hears the prayer of the righteous. Yehova amakhala kutali ndi anthu oyipa, koma amamva pemphero la anthu olungama.
30 The light of the eyes brings joy to the heart, and good news refreshes the bones. Kuwala kwa maso kumasangalatsa mtima ndipo uthenga wabwino umalimbitsa munthu.
31 The ear that listens to life-giving correction will dwell among the wise. Womvera mawu a chidzudzulo amene apatsa moyo adzakhala pakati pa anthu anzeru.
32 Whoever ignores instruction despises himself, but whoever listens to correction gains understanding. Amene amanyoza mwambo amadzinyoza yekha, koma womvera mawu a chidzudzulo amapeza nzeru zomvetsa zinthu.
33 The fear of our Father is the instruction of wisdom, and humility comes before honor. Kuopa Yehova kumaphunzitsa munthu nzeru, ndipo kudzichepetsa ndi ulemu chili patsogolo ndi kudzichepetsa.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]