Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 19 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Better is a poor person who walks in his integrity than one whose words are crooked and is a fool. Ndi wabwino munthu wosauka amene amayenda mu ungwiro, aposa munthu wopusa woyankhula zokhota.
2 Also, desire without knowledge is not good, and whoever acts in haste misses the way. Si bwino kuti munthu akhale wopanda nzeru; ndipo munthu woyenda mofulumira amaphonya njira.
3 A person's own foolishness ruins his way, yet his heart rages against our Father. Uchitsiru wa munthu umamubweretsera zovuta, mtima wake umakwiyira Yehova.
4 Wealth adds many friends, but the poor is separated from his friend. Chuma chimachulukitsa abwenzi; koma munthu wosauka bwenzi lake limamuthawa.
5 A false witness will not go unpunished, and one who breathes out lies will not escape. Mboni yonama sidzalephera kulangidwa; ndipo iye amene amanena mabodza sadzapulumuka.
6 Many seek the favor of a generous person, and everyone is a friend to one who gives gifts. Anthu ambiri amafuna munthu wopatsa kuti awakomere mtima, ndipo munthu amene amapereka mphatso ndi bwenzi la munthu aliyense.
7 All the brothers of a poor person hate him; how much more do his friends keep far from him! He calls after them, but they are gone. Ngati munthu wosauka abale ake omwe amadana naye, nanji abwenzi ake tsono! Iwo adzamuthawa kupita kutali. Amayesa kuwatsatira mowapembedza koma iwo samapezeka konse.
8 Whoever gets wisdom loves his own soul; whoever guards understanding will find good. Iye amene amapeza nzeru ndiye kuti amakonda moyo wake. Wosamalitsa kukhala wanzeru, zinthu zimamuyendera bwino.
9 A false witness will not go unpunished, and one who breathes out lies will perish. Mboni yonama sidzalephera kulangidwa, ndipo iye amene amanena mabodza adzawonongeka.
10 Luxury is not fitting for a fool—much less for a servant to rule over princes. Nʼkosayenera kuti chitsiru chizikhala ndi moyo wamanyado, nanjinso kuti kapolo azilamulira akalonga!
11 The good sense of a person makes him slow to anger, and it is his glory to overlook an offense. Nzeru zimapangitsa munthu kukhala wosakwiya msanga; ulemerero wake uli posalabadira kuchitiridwa zoyipa.
12 A king's wrath is like the roaring of a lion, but his favor is like dew on the grass. Mkwiyo wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango, koma kukoma mtima kwake kuli ngati mame pa udzu.
13 A foolish son is ruin to his father, and a wife's quarreling is a continual dripping. Mwana wopusa ndiye tsoka la abambo ake ndipo mkazi wolongolola ndi wotopetsa ngati mvula yamvumbi.
14 House and wealth are an inheritance from one's ancestors, but a prudent wife is from our Father. Nyumba ndi chuma ndiye cholowa chochokera kwa makolo; koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Yehova.
15 Laziness casts into deep sleep, and an idle person will go hungry. Ulesi umagonetsa tulo tofa nato ndipo munthu wosatakataka amakhala ndi njala.
16 Whoever keeps the commandment keeps his life; whoever despises his ways will die. Amene amamvera malangizo amasunga moyo wake, koma amene sasamala malamulo a Yehova adzafa.
17 Whoever is generous to the poor lends to our Father, and our Father will repay him for his deed. Amene amakomera mtima osauka amachita ngati wakongoletsa Yehova, ndipo Yehovayo ndiye adzamubwezere.
18 Discipline your son while there is hope, and do not set your heart on his destruction. Langa mwana wako, chiyembekezo chikanalipo; ngati sutero udzawononga moyo wake.
19 A person of great wrath must pay the penalty; for if you rescue him, you will only have to do it again. Munthu waukali woopsa ayenera kulandira chilango; pakuti akamulekelera ndiye zidzayipa kuposa kale.
20 Listen to counsel and accept discipline, that you may gain wisdom in the days to come. Mvera uphungu ndipo landira malangizo; pa mapeto pake udzakhala wanzeru.
21 Many are the plans in a person's heart, but it is the counsel of our Father that will stand. Munthu amakonzekera zambiri mu mtima mwake, koma cholinga cha Yehova ndiye chidzachitike.
22 What is desired in a person is covenant love, and a poor person is better than a liar. Chimene munthu amafuna ndi chikondi chosatha; nʼkwabwino kukhala wosauka kusiyana ndi kukhala wabodza.
23 The fear of our Father leads to life, and whoever has it rests satisfied, untouched by harm. Kuopa Yehova kumabweretsa moyo; wotereyo amakhala mu mtendere; ndiye kuti choyipa sichidzamugwera.
24 The sluggard buries his hand in the dish and will not even bring it back to his mouth. Munthu waulesi amapisa dzanja lake mʼmbale; koma sangathe kufikitsa dzanja lakelo pakamwa pake.
25 Strike a mocker, and the simple will learn prudence; reprove a person of understanding, and he will gain knowledge. Menya munthu wonyoza, ndipo anthu opanda nzeru adzachenjererapo; dzudzula munthu wozindikira zinthu, ndipo iye adzapezapo chidziwitso.
26 Whoever does violence to his father and drives away his mother is a son who brings shame and disgrace. Mwana wochita ndewu ndi abambo ake ndi kuthamangitsa amayi ake, ndi mwana wochititsa manyazi ndi wonyozetsa.
27 Stop listening to instruction, my son, and you will stray from the words of knowledge. Mwana wanga, ukaleka kumvera malangizo, udzapatukana ndi mawu opatsa nzeru.
28 A worthless witness mocks at justice, and the mouth of the wicked gulps down wickedness. Mboni yopanda pake imanyoza cholungama, ndipo pakamwa pa anthu oyipa pamameza zoyipa.
29 Punishment is prepared for mockers, and beatings for the backs of fools. Chilango chakonzedwa kale kuti chigwere anthu oyipa, ndipo mkwapulo wakonzedwa kale kuti ukwapule misana ya anthu opusa.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]