Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 20 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Wine is a mocker, strong drink a brawler, and whoever staggers under it is not wise. Vinyo amachititsa munthu kukhala wonyoza ndipo chakumwa choledzeretsa chimachititsa munthu kukhala wolongolola; aliyense wosochera nazo zimenezi alibe nzeru.
2 The terror of a king is like the growl of a lion; whoever provokes him to anger forfeits his own life. Ukali wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango; amene amawuputa mkwiyowo amataya moyo wake.
3 It is an honor for a person to keep clear of strife, but every fool is quick to quarrel. Nʼchaulemu kwa munthu kupewa mikangano, koma chitsiru chilichonse chimafulumira kulongolola.
4 A lazy person will not plow in autumn; so at harvest he looks for a crop and finds nothing. Munthu waulesi satipula mʼmunda pa nthawi yoyenera; kotero pa nthawi yokolola adzafunafuna zinthu koma sadzapeza kanthu kalikonse.
5 The purposes of a person's heart are deep waters, but one who has understanding draws them out. Zolinga za mtima wa munthu zili ngati madzi akuya, munthu womvetsa zinthu ndiye yekha angawatunge.
6 Many a person proclaims his own loyal love, but a faithful one—who can find? Anthu ambiri amayankhula za kukhulupirika kwawo, koma munthu wokhulupirika angamupeze ndani?
7 The righteous walk in their integrity; blessed are their children after them! Munthu wolungama amakhala ndi makhalidwe abwino; odala ndi ana ake amene amatsanzira moyo wake.
8 A king seated on the throne of judgment winnows out all evil with his eyes. Mfumu ikhala pa mpando wake wa chiweruzo, imapeta ndi maso ake anthu onse oyipa.
9 Who can say, "I have kept my heart pure; I am cleansed from my sin"? Ndani amene anganene kuti, “Ndawuyeretsa mtima wanga; ndilibe tchimo lililonse?”
10 Unequal weights and unequal measures—our Father detests them both. Masikelo ndi miyeso ya zinthu imene ili yachinyengo zonsezi Yehova zimamunyansa.
11 Even a child is known by his actions, by whether his conduct is pure and upright. Ngakhale mwana amadziwika ndi zochita zake, ngati zochita zake zili zoyera ndi zoyenera.
12 The hearing ear and the seeing eye—our Father made them both. Makutu amene amamva ndi maso amene amaona, zonsezi anazilenga ndi Yehova.
13 Do not love sleep, or you will grow poor; open your eyes, and you will have plenty of bread. Usakonde tulo ungasauke; khala maso ndipo udzakhala ndi chakudya chambiri.
14 "Worthless, worthless!" says the buyer—then off he goes and boasts of his bargain. Munthu wogula chinthu amati, “Sichabwino, sichabwino.” Koma akagula nʼkuchokapo amayamba kudzitama.
15 There is gold and an abundance of jewels, but lips that speak knowledge are a rare treasure. Pali golide ndi miyala yamtengowapatali, koma milomo yoyankhula zanzeru ndi yamtengowapatali koposa zonsezi.
16 Take the garment of one who puts up security for a stranger; hold it as a pledge when he does so for foreigners. Utenge chovala cha munthu amene waperekera mlendo chikole; kuti chikhale chikole chako chifukwa waperekera chikole munthu wachilendo.
17 Bread gained by deceit tastes sweet, but afterward the mouth is full of gravel. Chakudya chochipeza mwachinyengo chimukomera munthu, koma pa mapeto pake chimasanduka ngati mchenga mʼkamwa mwake.
18 Plans are established by counsel; so wage war only with wise guidance. Zokonzekera zimapindula utafunsira uphungu; ndipo usanamenye nkhondo yamba wapempha malangizo oyenera.
19 A gossip betrays a confidence; so do not keep company with a babbler. Amene amanka nanena miseche amawulula zachinsinsi. Choncho usamagwirizane naye munthu woyankhula zopusayo.
20 Whoever curses his father or mother—his lamp will be snuffed out in deepest darkness. Ngati munthu atemberera abambo ake kapena amayi ake, moyo wake udzazimitsidwa ngati nyale mu mdima wandiweyani.
21 An inheritance gained too quickly at the start will not be blessed in the end. Cholowa chochipeza mofulumira poyamba, sichidzakhala dalitso pa mapeto pake.
22 Do not say, "I will pay back evil for evil." Wait for our Father, and he will deliver you. Usanene kuti, “Ine ndidzabwezera choyipa chimenechi!” Dikira Yehova, ndipo Iye adzakupulumutsa.
23 Our Father detests unequal weights, and dishonest scales are no good. Miyeso yosintha imamunyansa Yehova; ndipo masikelo onyenga si abwino.
24 A person's steps are directed by our Father; how then can anyone understand his own way? Mayendedwe a munthu amawalamulira ndi Yehova, tsono munthu angadziwe bwanji njira yake?
25 It is a trap to rashly dedicate something and only later reconsider the vow. Ndi msampha kwa munthu kuyankhula mofulumira kuti “Chinthu ichi nʼchopatulika kwa Yehova,” popeza mwina atha kusintha maganizo utalumbira kale.
26 A wise king winnows out the wicked and drives the threshing wheel over them. Mfumu ya nzeru imapeta kwathunthu anthu oyipa.
27 The human spirit is the lamp of our Father, searching every inmost part. Mpweya wa munthu uli ngati nyale ya Yehova; imafufuza ziwalo zake zonse zamʼkati.
28 Loyal love and faithfulness preserve a king; by loyal love his throne is upheld. Kukoma mtima ndi kukhulupirika ndizo zimasunga mfumu; chilungamo chimalimbikitsa mpando wake waufumu.
29 The glory of the young is their strength, but the splendor of the old is gray hair. Ulemerero wa achinyamata uli mu mphamvu zawo, imvi ndi ulemerero wa anthu okalamba.
30 Wounding blows scrub away evil, and beatings cleanse the inmost parts. Mikwingwirima yopweteka ndiyo imachotsa zoyipa, ndipo mikwapulo ndiyo imachotsa zamʼkatikati mwa munthu.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]