Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 21 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 The king's heart is a stream of water in our Father's hand; he turns it wherever he pleases. Mtima wa mfumu uli ngati mtsinje wamadzi mʼdzanja la Yehova; Iye amautsongolera pa chilichonse chimene akufuna.
2 Every way of a person seems right in their own eyes, but our Father weighs the heart. Makhalidwe a munthu amaoneka olungama kwa mwini wakeyo, koma Yehova ndiye amayesa mtima wake.
3 To do what is right and just is more pleasing to our Father than sacrifice. Za chilungamo ndi zolondola ndi zomwe zimakondweretsa Yehova kuposa kupereka nsembe.
4 Haughty eyes and a proud heart—the lamp of the wicked—are sin. Maso odzikuza ndi mtima wonyada, zimatsogolera anthu oyipa ngati nyale nʼchifukwa chake amachimwa.
5 The plans of the diligent lead surely to abundance, but all who are hasty end up in poverty. Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa zinthu zake; koma aliyense wochita zinthu mofulumira amadzakhala wosauka.
6 Making a fortune by a lying tongue is a fleeting vapor, a deadly trap. Chuma chochipeza ndi mawu onyenga ndi chosakhalitsa ndipo chimakola anthu mu msampha wa imfa.
7 The violence of the wicked will drag them away, because they refuse to do what is just. Chiwawa cha anthu oyipa chidzawawononga, pakuti iwo amakana kuchita zolungama.
8 The way of the guilty is crooked, but the conduct of the pure is upright. Njira ya munthu wolakwa ndi yokhotakhota, koma makhalidwe a munthu wosalakwa ndi olungama.
9 Better to live in a corner of the roof than in a shared house with a quarrelsome wife. Nʼkwabwino kukhala wekha pa ngodya ya denga la nyumba, kuposa kukhala mʼnyumba pamodzi ndi mkazi wolongolola.
10 The soul of the wicked craves evil; their neighbor finds no mercy in their eyes. Munthu woyipa amalakalaka zoyipa; sachitira chifundo mnansi wake wovutika.
11 When a mocker is punished, the simple grow wise; when the wise are instructed, they gain knowledge. Munthu wonyoza akalangidwa, anthu opusa amapeza nzeru; koma munthu wanzeru akalangizidwa, amapeza chidziwitso.
12 Our Father, the Righteous One, observes the house of the wicked and brings the wicked to ruin. Zolingalira za munthu woyipa nʼzosabisika pamaso pa Yehova, ndipo Iye adzawononga woyipayo.
13 Whoever shuts their ears to the cry of the poor will also cry out and not be answered. Amene atsekera mʼkhutu mwake wosauka akamalira, nayenso adzalira koma palibe adzamuyankhe.
14 A gift given in secret soothes anger, and a bribe slipped into the cloak calms strong wrath. Mphatso yoperekedwa mseri imathetsa mkwiyo, ndipo chiphuphu choperekedwa mobisa chimathetsa mphamvu ya ukali woopsa.
15 When justice is done, it is a joy to the righteous but terror to those who do evil. Chilungamo chikachitika anthu olungama amasangalala, koma anthu oyipa amaopsedwa nazo.
16 A person who strays from the way of understanding will rest in the assembly of the dead. Munthu amene amachoka pa njira ya anthu anzeru adzapezeka mʼgulu la anthu akufa.
17 Whoever loves pleasure will become poor; whoever loves wine and oil will never grow rich. Aliyense wokonda zisangalalo adzasanduka mʼmphawi, ndipo wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera.
18 The wicked become a ransom for the righteous, and the treacherous for the upright. Anthu oyipa adzakhala chowombolera cha anthu olungama ndipo osakhulupirika chowombolera anthu olungama mtima.
19 Better to live in a desert land than with a quarrelsome and complaining wife. Nʼkwabwino kukhala mʼchipululu kuposa kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wopsa mtima msanga.
20 Precious treasure and oil are in the home of the wise, but a fool devours all he has. Munthu wanzeru samwaza chuma chake, koma wopusa amachiwononga.
21 Whoever pursues righteousness and faithful love will find life, righteousness, and honor. Amene amatsata chilungamo ndi kukhulupirika, amapeza moyo ndi ulemerero.
22 A wise person scales the city of the mighty and brings down the stronghold they trust in. Munthu wanzeru amagonjetsa mzinda wa anthu amphamvu ndi kugwetsa linga limene iwo amalidalira.
23 Whoever guards their mouth and tongue keeps themselves out of trouble. Amene amagwira pakamwa pake ndi lilime lake sapeza mavuto.
24 "Mocker" is the name of the proud and arrogant who acts with outrageous insolence. Munthu wonyada ndi wodzikuza amamutcha, “Mnyodoli,” iye amachita zinthu modzitama kwambiri.
25 The craving of a lazy person kills him, for his hands refuse to work. Chilakolako cha munthu waulesi chidzamupha yekha chifukwa manja ake amangokhala goba osagwira ntchito.
26 All day long the craving grows, but the righteous give and do not hold back. Tsiku lonse anthu oyipa amasirira zambiri, koma anthu olungama amapereka mowolowamanja.
27 The sacrifice of the wicked is detestable—how much more when brought with evil intent. Nsembe ya anthu oyipa imamunyansa Yehova, nanji akayipereka ndi cholinga choyipa!
28 A false witness will perish, but whoever listens will testify with lasting effect. Mboni yonama idzawonongeka, koma mawu a munthu wakumva adzakhala nthawi zonse.
29 The wicked put on a bold face, but the upright give thought to their ways. Munthu woyipa amafuna kudzionetsa ngati wolimba mtima, koma munthu wowongoka amaganizira njira zake.
30 There is no wisdom, no understanding, no counsel that can stand against our Father. Palibe nzeru, palibe kumvetsa bwino, palibenso uphungu, zimene zingapambane Yehova.
31 The horse is made ready for the day of battle, but victory belongs to our Father. Kavalo amamukonzera tsiku la nkhondo, koma ndi Yehova amene amapambanitsa.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]