Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 22 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 A good name is to be chosen rather than great riches, and favor is better than silver or gold. Mbiri yabwino ndi yofunika kuposa chuma chambiri; kupeza kuyanja nʼkwabwino kuposa siliva kapena golide.
2 The rich and the poor meet together; our Father is the Maker of them all. Wolemera ndi wosauka ndi ofanana; onsewa anawalenga ndi Yehova.
3 The prudent sees danger and takes cover, but the simple keep going and pay the price. Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala, koma munthu wopusa amangopitirira ndipo amadzanongʼoneza bondo.
4 The reward for humility and the fear of our Father is riches and honor and life. Mphotho ya munthu wodzichepetsa ndi woopa Yehova ndi chuma, ulemu ndi moyo.
5 Thorns and snares lie in the path of the crooked; whoever guards his soul stays far from them. Mʼnjira za anthu oyipa muli minga ndi misampha, koma amene amasala moyo wake adzazipewa zonsezo.
6 Train up a child in the way he should go, and even when he is old he will not depart from it. Mwana muzimuphunzitsa njira yake, ndipo akadzakalamba sadzachokamo.
7 The rich rules over the poor, and the borrower is slave to the lender. Wolemera amalamulira wosauka, ndipo wokongola zinthu amakhala kapolo wa womukongozayo.
8 Whoever sows injustice will reap calamity, and the rod of his fury will fail. Amene amafesa zoyipa amakolola mavuto, ndipo ndodo yaukali wake idzathyoka.
9 Whoever has a generous eye will be blessed, for he shares his bread with the poor. Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsika, pakuti iye amagawana chakudya chake ndi anthu osauka.
10 Drive out the scoffer, and strife goes with him; quarreling and abuse will cease. Chotsani munthu wonyoza, ndipo kukangana kudzatha; mapokoso ndi zonyoza zidzaleka.
11 Whoever loves a pure heart and speaks graciously will have the king as his friend. Amene amakonda kukhala woyera mtima ndi kumayankhula mawu abwino, adzakhala bwenzi la mfumu.
12 The eyes of our Father keep watch over knowledge, but he overturns the words of the traitor. Maso a Yehova amakhala pa anthu odziwa bwino zinthu, koma Iye adzalepheretsa mawu a anthu osakhulupirika.
13 The lazy person says, "There is a lion outside! I will be killed in the streets!" Munthu waulesi amati, “Kunjaku kuli mkango. Ine ndidzaphedwa mʼmisewu!”
14 The mouth of forbidden women is a deep pit; whoever draws our Father's anger will fall into it. Pakamwa pa mkazi wachigololo pali ngati dzenje lozama; amene Yehova wamukwiyira adzagwamo.
15 Foolishness is bound up in the heart of a child, but the rod of discipline drives it far away. Uchitsiru umakhala mu mtima mwa mwana, koma ndodo yomulangira mwanayo idzachotsa uchitsiruwo.
16 Whoever oppresses the poor to enrich himself, or gives to the rich, will come only to poverty. Amene amapondereza anthu osauka kuti awonjezere chuma chake, ndiponso amene amapereka mphatso kwa anthu olemera onsewa adzasauka.
17 Listen carefully to the words of the wise, and apply your heart to my knowledge, Utchere khutu lako ndipo umvere mawu anzeru; uyike mtima wako pa zimene ndikukuphunzitsa kuti udziwe.
18 for it will be pleasant if you keep them within you, if all of them are ready on your lips. Zidzakhala zokondweretsa ngati uzisunga mu mtima mwako ndi wokonzeka kuziyankhula.
19 So that your trust may be in our Father, I have made them known to you today, even to you. Ndakuphunzitsa zimenezi lero koma makamaka uziopa Yehova.
20 Have I not written for you thirty sayings of counsel and knowledge, Kodi suja ndinakulembera malangizo makumi atatu okuchenjeza ndi okupatsa nzeru,
21 to teach you what is right and true, so that you may give a true answer to those who sent you? malangizo okudziwitsa zolungama ndi zoona ndi kuti ukawayankhe zoona amene akutumawo?
22 Do not rob the poor because he is poor, or crush the afflicted at the gate, Mʼmphawi usamubere chifukwa ndi osauka, ndipo usawapondereze anthu osowa mʼbwalo la milandu,
23 for our Father will plead their cause and will rob of life those who rob them. pakuti Yehova adzawateteza pa mlandu wawo ndipo adzalanda moyo onse amene amawalanda iwo.
24 Do not befriend a man given to anger, and do not go with a hot-tempered man, Usapalane naye ubwenzi munthu wosachedwa kupsa mtima ndipo usayanjane ndi munthu amene sachedwa kukwiya
25 or you will learn his ways and entangle yourself in a snare. kuopa kuti iwe ungadzaphunzire njira zake ndi kukodwa mu msampha.
26 Do not be one of those who give pledges, who put up security for debts. Usakhale munthu wopereka chikole kapena kukhala mboni pa ngongole;
27 If you have nothing to pay with, why should your bed be taken from under you? ngati ulephera kupeza njira yolipirira adzakulanda ngakhale bedi lako lomwe.
28 Do not move the ancient boundary stone that your fathers set up. Usasunthe mwala wamʼmalire akalekale amene anayikidwa ndi makolo ako.
29 Do you see a man skillful in his work? He will stand before kings; he will not stand before ordinary men. Kodi ukumuona munthu waluso pa ntchito yake? Iye adzatumikira mafumu; sadzatumikira anthu wamba.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]