Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 23 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 When you sit down to dine with a ruler, consider carefully what is before you, Ngati ukhala pansi kuti udye pamodzi ndi wolamulira, uyangʼane bwino zimene zili pamaso pako,
2 and put a knife to your throat if you are a person ruled by appetite. ngati ndiwe munthu wadyera udziletse kuti usaonetse dyera lakolo.
3 Do not crave his delicacies, for they are deceptive food. Usasirire zakudya zake, pakuti zimenezo ndi zakudya zachinyengo.
4 Do not wear yourself out to get rich; have the wisdom to restrain yourself. Usadzitopetse wekha ndi kufuna chuma, ukhale ndi nzeru ya kudziretsa.
5 The moment you look at wealth, it is gone, for it suddenly sprouts wings and flies off toward the heavens like an eagle. Ukangoti wachipeza chumacho uwona posachedwa kuti palibepo. Chumacho chimachita ngati chamera mapiko mwadzidzidzi ndi kuwuluka kunka kumwamba ngati chiwombankhanga.
6 Do not eat the bread of a stingy man, and do not crave his delicacies, Usadye chakudya cha munthu waumbombo, usalakalake zakudya zake zokoma;
7 for he is the kind of man who keeps counting the cost. "Eat and drink!" he says to you, but his heart is not with you. paja iye ndi munthu amene nthawi zonse amaganizira za mtengo wake ngakhale amati kwa iwe, “Idya ndi kumwa,” koma sakondweretsedwa nawe.
8 You will vomit up the little you have eaten and will have wasted your pleasant words. Udzasanza zimene wadyazo ndipo mawu ako woyamikira adzapita pachabe.
9 Do not speak in the hearing of a fool, for he will despise the wisdom of your words. Usayankhule munthu wopusa akumva, pakuti adzanyoza mawu ako anzeru.
10 Do not move an ancient boundary stone or encroach on the fields of the fatherless, Usasunthe mwala wa mʼmalire akalekale kapena kulowerera mʼminda ya ana amasiye,
11 for their Redeemer is strong; our Father will take up their cause against you. paja Mpulumutsi wawo ndi wamphamvu; iye adzawateteza pa milandu yawo kutsutsana nawe.
12 Apply your heart to instruction and your ears to words of knowledge. Mtima wako uzikhala pa malangizo ndipo makutu ako azimvetsera mawu a chidziwitso.
13 Do not withhold discipline from a child; if you strike him with the rod, he will not die. Usaleke kumulangiza mwana; ngati umulanga ndi chikwapu sadzafa.
14 Strike him with the rod, and you will deliver his soul from the grave. Ukamukwapula ndi tsatsa udzapulumutsa moyo wake.
15 My son, if your heart is wise, my own heart will be glad as well. Mwana wanga, ngati mtima wako ukhala wanzeru, inenso mtima wanga udzakondwera.
16 My inmost being will rejoice when your lips speak what is right. Mtima wanga udzakondwera pamene ndidzakumva ukuyankhula zolungama.
17 Do not let your heart envy sinners, but continue in the fear of our Father all day long. Mtima wako usachite nsanje ndi anthu ochimwa, koma uziopa Yehova tsiku ndi tsiku.
18 Surely there is a future, and your hope will not be cut off. Ndithu za mʼtsogolo zilipo ndipo chiyembekezo chakocho sichidzalephereka.
19 Hear, my son, and be wise, and keep your heart on the right road. Tamvera mwana wanga, ndipo ukhale wanzeru, mtima wako uwuyendetse mʼnjira yabwino.
20 Do not be among those who get drunk on wine or those who gorge themselves on meat, Usakhale pakati pa anthu amene amaledzera kapena pakati pa anthu amene amadya nyama mwadyera.
21 for the drunkard and the glutton will come to poverty, and drowsiness will clothe them in rags. Paja anthu oledzera ndi adyera amadzakhala amphawi ndipo aulesi adzavala sanza.
22 Listen to your father, who gave you life, and do not despise your mother when she is old. Mvera abambo ako amene anakubala, usanyoze amayi ako pamene akalamba.
23 Buy truth and do not sell it; buy wisdom, instruction, and understanding. Gula choonadi ndipo usachigulitse; ugulenso nzeru, mwambo ndiponso kumvetsa zinthu bwino.
24 The father of a righteous child will greatly rejoice; whoever fathers a wise son will delight in him. Abambo a munthu wolungama ali ndi chimwemwe chachikulu; Wobala mwana wanzeru adzakondwera naye.
25 Let your father and mother be glad; let her who gave you birth rejoice. Abambo ndi amayi ako asangalale; amene anakubereka akondwere!
26 My son, give me your heart, and let your eyes delight in my ways. Mwana wanga, undikhulupirire ndipo maso ako apenyetsetse njira zanga.
27 For a prostitute is a deep pit, and an adulterous woman is a narrow well. Paja mkazi wachiwerewere ali ngati dzenje lozama; ndipo mkazi woyendayenda ali ngati chitsime chopapatiza.
28 She lies in wait like a robber and leads many men into faithlessness. Amabisala ngati mbala yachifwamba, ndipo amuna amakhala osakhulupirika chifukwa cha iyeyu.
29 Who has misery? Who has sorrow? Who has strife? Who has complaints? Who has wounds for no reason? Who has bleary eyes? Ndani ali ndi tsoka? Ndani ali ndi chisoni? Ndani ali pa mkangano? Ndani ali ndi madandawulo? Ndani ali ndi zipsera zosadziwika uko zachokera? Ndani ali ndi maso ofiira?
30 Those who linger long over wine, those who go to sample bowls of mixed wine. Ndi amene amakhalitsa pa mowa, amene amapita nalawa vinyo osakanizidwa.
31 Do not gaze at wine while it is red, while it sparkles in the cup and goes down smoothly. Usatengeke mtima ndi kufiira kwa vinyo, pamene akuwira mʼchikho pamene akumweka bwino!
32 In the end it bites like a serpent and stings like a viper. Potsiriza pake amaluma ngati njoka, ndipo amajompha ngati mphiri.
33 Your eyes will see strange things, and your heart will utter twisted things. Maso ako adzaona zinthu zachilendo ndipo maganizo ndi mawu ako adzakhala osokonekera.
34 You will be like one lying down in the heart of the sea, like one lying on the top of a ship's mast. Udzakhala ngati munthu amene ali gone pakati pa nyanja, kapena ngati munthu wogona pa msonga ya mlongoti ya ngalawa.
35 "They struck me, but I felt no pain; they beat me, but I did not know it. When will I wake up? I will look for another drink." Iwe udzanena kuti, “Anandimenya, koma sindinapwetekedwe! Andimenya koma sindinamve kanthu! Kodi ndidzuka nthawi yanji? Ndiye ndifunefunenso vinyo wina.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]