Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 24 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Do not envy evil men, and do not desire to be with them, Usachitire nsanje anthu oyipa, usalakalake kuti uzikhala nawo,
2 for their hearts plot violence, and their lips speak of trouble. pakuti mitima yawo imalingalira chiwawa, ndipo pakamwa pawo pamayankhula zoyambitsa mavuto.
3 By wisdom a house is built, and by understanding it is established; Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru, ndipo imakhazikika ndi anthu odziwa zinthu;
4 and by knowledge its rooms are filled with all precious and pleasant riches. Munthu wodziwa zinthu angathe kudzaza zipinda zake ndi chuma chamtengowapatali ndiponso chabwino.
5 A wise man is full of strength, and a man of knowledge increases his power, Munthu wodziwa zinthu ali ndi mphamvu yayikulu kuposa munthu wanyonga zambiri, ndipo munthu wachidziwitso amaposa munthu wamphamvu.
6 for by wise guidance you can wage your war, and victory comes through many counselors. Pafunika malangizo kuti ukamenye nkhondo. Pakakhala aphungu ambiri kupambana kumakhalapo.
7 Wisdom is too high for a fool; at the gate, he has nothing to say. Nzeru ndi chinthu chapatali kwambiri kwa chitsiru; chilibe choti chiyankhule pabwalo la milandu pa chipata.
8 Whoever plans to do evil will be called a schemer. Amene amakonzekera kuchita zoyipa adzatchedwa mvundulamadzi.
9 A fool's scheming is sin, and the scoffer is detestable to people. Kukonzekera kuchita za uchitsiru ndi tchimo, ndipo munthu wonyoza amanyansa anthu.
10 If you falter in a time of trouble, your strength is small. Ngati utaya mtima nthawi ya mavuto ndiye kuti mphamvu yako ndi yochepadi!
11 Rescue those being taken away to death, and hold back those stumbling toward the slaughter. Uwapulumutse amene akutengedwa kuti akaphedwe; uwalanditse amene akuyenda movutika kupita kokaphedwa.
12 If you say, "Look, we did not know this," does not he who weighs the heart perceive it? Does not he who watches over your soul know it? And will he not repay each person according to his deeds? Ukanena kuti, “Koma ife sitinadziwe kanthu za izi,” kodi Iye amene amasanthula mtima sazindikira zimenezi? Kodi Iye amene amateteza moyo wako sazidziwa zimenezi? Kodi Iye sadzalipira munthu malingana ndi ntchito zake?
13 My son, eat honey, for it is good, and the honeycomb's drippings are sweet to your taste. Mwana wanga, uzidya uchi popeza ndi wabwino; uchi wochokera mʼchisa cha njuchi ndi wokoma ukawulawa.
14 Know that wisdom is just like this to your soul; if you find it, there is a future, and your hope will not be cut off. Udziwe kuti nzeru ndi yoteronso pa moyo wako; ngati uyipeza nzeruyo, zinthu zidzakuyendera bwino mʼtsogolo, ndipo chiyembekezo chako sichidzapita pachabe.
15 Do not lie in wait, you wicked man, against the home of the righteous; do not destroy his resting place, Usachite zachifwamba nyumba ya munthu wolungama ngati munthu woyipa. Usachite nayo nkhondo nyumba yake;
16 for though the righteous falls seven times, he rises again, but the wicked stumble in disaster. paja munthu wolungama akagwa kasanu nʼkawiri amadzukiriranso. Koma woyipa adzathedwa tsoka likadzawafikira.
17 Do not rejoice when your enemy falls, and do not let your heart be glad when he stumbles, Usamakondwera ndi kugwa kwa mdani wako. Mtima wako usamasangalale iye akapunthwa.
18 lest our Father see it and be displeased, and turn his anger away from him. Kuopa kuti Yehova ataziona zimenezi nayipidwa nazo, angaleke kukwiyira mdaniyo.
19 Do not fret because of evildoers, and do not envy the wicked, Usavutike mtima chifukwa cha anthu ochita zoyipa kapena kuchitira nsanje anthu oyipa,
20 for the evil man has no future; the lamp of the wicked will be snuffed out. paja munthu woyipa alibe tsogolo. Moyo wa anthu oyipa adzawuzimitsa ngati nyale.
21 My son, fear our Father and the king, and do not join with those who rebel against them, Mwana wanga, uziopa Yehova ndi mfumu, ndipo usamagwirizana ndi anthu owachitira mwano,
22 for their disaster will rise suddenly, and who knows the ruin that both of them can bring? awiri amenewa amagwetsa tsoka mwadzidzidzi. Ndani angadziwe mavuto amene angagwetse?
23 These also are sayings of the wise: Showing partiality in judgment is not good. Malangizo enanso a anthu anzeru ndi awa: Kukondera poweruza mlandu si chinthu chabwino:
24 Whoever says to the guilty, "You are innocent," peoples will curse him and nations will denounce him, Aliyense amene amawuza munthu wolakwa kuti, “Iwe ndi munthu wosalakwa,” anthu a mitundu yonse adzamutemberera, ndi mitundu ya anthu idzayipidwa naye.
25 but it will go well for those who convict the guilty, and a rich blessing will come upon them. Koma olanga anthu oyipa zinthu zidzawayendera bwino ndipo madalitso ochuluka adzakhala pa iwo.
26 An honest answer is like a kiss on the lips. Woyankhula mawu owona ndiye amaonetsa chibwenzi chenicheni.
27 Prepare your work outside, get your fields ready, and after that build your house. Ugwiriretu ntchito zako zonse, makamaka za ku munda ndipo pambuyo pake uyambe kumanga nyumba.
28 Do not be a witness against your neighbor without cause; would you deceive with your lips? Usakhale mboni yotsutsa mnzako popanda chifukwa, kapena kugwiritsa ntchito pakamwa pako kunena zachinyengo.
29 Do not say, "I will do to him as he did to me; I will pay the man back for what he has done." Usanene kuti, “Ine ndidzamuchitira iye monga momwe wandichitira ine; ndidzamubwezera munthu ameneyo zimene anandichitira.”
30 I passed by the field of a lazy man, by the vineyard of someone lacking sense, Ndinkayenda mʼmbali mwa munda wa munthu waulesi ndinadutsa munda wamphesa wa munthu wopanda nzeru.
31 and there it was, all overgrown with thorns; the ground was covered with weeds, and its stone wall was broken down. Ndinapeza kuti paliponse mʼmundamo munali mutamera minga, mʼnthaka imeneyo munali mutamera khwisa, ndipo mpanda wake wamiyala unali utawonongeka.
32 Then I looked and took it to heart; I saw and received instruction. Tsono nditaona ndinayamba kuganizira mu mtima mwanga ndipo ndinatolapo phunziro ili:
33 A little sleep, a little slumber, a little folding of the hands to rest, Ukati, “Bwanji ndigone pangʼono,” kapena “Ndiwodzereko pangʼono,” kapenanso “Ndipinde manja pangʼono kuti ndipumule,”
34 and poverty will come upon you like a robber, and scarcity like an armed man. umphawi udzafika pa iwe ngati mbala ndipo usiwa udzakupeza ngati munthu wachifwamba.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]