Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 25 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 These also are proverbs of Solomon, which the men of Hezekiah king of Judah copied out. Iyi ndi miyambo inanso ya Solomoni, imene anthu a Hezekiya mfumu ya ku Yuda analemba.
2 It is the glory of our Father to conceal a matter, but the glory of kings to search a matter out. Ulemerero wa Mulungu uli pa kubisa zinthu; ulemerero wa mafumu uli pa kufufuza zinthuzo.
3 As the heavens are high and the earth is deep, so the heart of kings is unsearchable. Monga momwe kwatalikira kumwamba ndi momwe kulili kuzama kwa dziko lapansi, ndi momwemonso alili maganizo a mfumu kusadziwika kwake.
4 Take away the dross from the silver, and a vessel comes forth for the refiner. Chotsa zoyipa mʼsiliva ndipo wosula adzapanga naye ziwiya.
5 Take away the wicked from before the king, and his throne will be established in righteousness. Chotsa munthu woyipa pamaso pa mfumu; ndipo ufumu wake udzakhazikika mu chilungamo.
6 Do not put yourself forward in the king's presence, and do not stand in the place of the great; Usamadzikuze ukakhala pamaso pa mfumu, ndipo usamakhale pamalo pa anthu apamwamba;
7 for it is better to be told, "Come up here," than to be put in a lower place in front of a noble you can see. paja ndi bwino kuti mfumu ichite kukuwuza kuti, “Bwera pamwamba pano,” kulekana ndi kuti ikuchititse manyazi chifukwa cha wina wokuposa. Chimene wachiona ndi maso ako,
8 Do not rush into a quarrel, for what will you do in the end when your neighbor puts you to shame? usafulumire kupita nacho ku bwalo la milandu nanga udzachita chiyani pa mapeto pake ngati mnansi wako adzakuchititsa manyazi?
9 Argue your case with your neighbor himself, but do not disclose another's secret, Kamba mlandu ndi mnansi wako, koma osawulula chinsinsi cha munthu wina
10 lest the one who hears it shame you, and your bad reputation never goes away. kuopa kuti wina akamva mawu ako adzakuchititsa manyazi ndipo mbiri yako yoyipa sidzatha.
11 A word spoken at the right moment is like apples of gold in settings of silver. Mawu amodzi woyankhulidwa moyenera ali ngati zokongoletsera zagolide mʼzotengera zasiliva.
12 Like a ring of gold or an ornament of fine gold is wise correction to a listening ear. Kwa munthu womvetsa bwino, kudzudzula kwa munthu wanzeru kuli ngati ndolo zagolide kapena chodzikongoletsera china cha golide wabwino kwambiri.
13 Like the cold of snow in the time of harvest is a faithful messenger to those who send him; he refreshes the soul of his masters. Wamthenga wodalirika ali ngati madzi ozizira pa nthawi yokolola kwa anthu amene amutuma; iye amaziziritsa mtima bwana wake.
14 Like clouds and wind without rain is one who boasts of a gift never given. Munthu wonyadira mphatso imene sayipereka ali ngati mitambo ndi mphepo yopanda mvula.
15 By patience a ruler is persuaded, and a soft tongue breaks bone. Kupirira ndiye kumagonjetsa mfumu, ndipo kufewa mʼkamwa kutha kumafatsitsa munthu wowuma mtima.
16 If you find honey, eat only enough, or you will have too much and vomit. Ngati upeza uchi, ingodya okukwanira, kuopa ungakoledwe nawo ndi kuyamba kusanza.
17 Don't visit your neighbor's house too often, or he will grow weary of you and hate you. Uzipita kamodzikamodzi ku nyumba ya mnzako ukawirikiza kupita, udzadana naye.
18 Like a club, a sword, and a sharp arrow is one who bears false witness against his neighbor. Munthu wochitira mnzake umboni wonama, ali ngati chibonga kapena lupanga kapena muvi wakuthwa.
19 Like a bad tooth or a foot out of joint is trust in a faithless person in time of trouble. Kudalira munthu wosankhulupirika pa nthawi ya mavuto, kuli ngati dzino lobowoka kapena phazi lolumala.
20 Like one who takes off a garment on a cold day, like vinegar poured on baking soda, is the one who sings songs to a heavy heart. Kuyimbira nyimbo munthu wachisoni kuli ngati kuvula zovala pa nyengo yozizira kapena kuthira mchere pa chilonda.
21 If your enemy is hungry, give him bread to eat, and if he is thirsty, give him water to drink; Ngati mdani wako ali ndi njala, mupatse chakudya kuti adye; ngati ali ndi ludzu mupatse madzi kuti amwe.
22 for you will heap coals of fire on his head, and our Father will reward you. Pochita izi, udzamusenzetsa makala a moto pa mutu pake, ndipo Yehova adzakupatsa mphotho.
23 The north wind brings forth rain, and a secretive tongue, angry looks. Monga momwe mphepo yampoto imabweretsera mvula, chonchonso mjedu umadzetsa mkwiyo.
24 It is better to live in a corner of the rooftop than in a shared house with a quarrelsome wife. Nʼkwabwino kukhala pa ngodya ya denga kuposa kukhala mʼnyumba ndi mkazi wolongolola.
25 Like cold water to a weary soul is good news from a distant land. Mthenga wabwino wochokera ku dziko lakutali ali ngati madzi ozizira kwa munthu waludzu.
26 Like a muddied spring or a polluted fountain is a righteous person who gives way before the wicked. Munthu wolungama amene amagonjera munthu woyipa ali ngati kasupe wodzaza ndi matope kapena chitsime cha madzi oyipa.
27 It is not good to eat too much honey, nor to seek your own glory. Sibwino kudya uchi wambiri, sibwinonso kudzifunira wekha ulemu.
28 Like a city broken into and left without walls is a person who has no control over his own spirit. Munthu amene samatha kudziretsa ali ngati mzinda umene adani awuthyola ndi kuwusiya wopanda malinga.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]