Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 26 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Like snow in summer and like rain at harvest, honor is not fitting for a fool. Ngati chisanu choti mbee nthawi yachilimwe kapena mvula nthawi yokolola, ndi momwe zilili ndi ulemu wowulandira chitsiru.
2 Like a fluttering sparrow or a darting swallow, an undeserved curse does not come to rest. Ngati timba wokhalira kuwuluka kapena namzeze wokhalira kuzungulirazungulira, ndi mmenenso limachitira temberero lopanda chifukwa, silichitika.
3 A whip for the horse, a bridle for the donkey, and a rod for the backs of fools. Mkwapulo ndi wokwapulira kavalo, chitsulo ndi cha mʼkamwa mwa bulu, choncho ndodo ndi yoyenera ku msana wa chitsiru.
4 Do not answer a fool according to his foolishness, or you yourself will be like him. Usayankhe chitsiru monga mwa uchitsiru wake, kuopa kuti ungadzakhale ngati chitsirucho.
5 Answer a fool according to his foolishness, or he will be wise in his own eyes. Koma nthawi zina umuyankhe monga mwa uchitsiru wake, kuopa kuti angamadziyese yekha wanzeru.
6 Whoever sends a message through a fool cuts off his own feet and drinks down violence. Kutuma chitsiru kuti akapereke uthenga kuli ngati kudzidula mapazi ndipo kumakuyitanira mavuto.
7 Like the legs of a lame man hanging useless is a proverb in the mouth of fools. Monga miyendo ya munthu wolumala imene ilibe mphamvu ndi mmene ulili mwambi mʼkamwa mwa chitsiru.
8 Like binding a stone in a sling is giving honor to a fool. Kupereka ulemu kwa chitsiru zili ngati kukulunga mwala mʼlegeni.
9 Like a thornbush in the hand of a drunkard is a proverb in the mouth of fools. Monga umachitira mtengo waminga wobaya mʼdzanja la chidakwa ndi mmene ulili mwambi mʼkamwa mwa chitsiru.
10 Like an archer who wounds everyone is one who hires a fool or hires any passerby. Munthu amene amalemba ntchito chitsiru chongoyendayenda, ali ngati woponya mivi amene angolasa anthu chilaselase.
11 As a dog returns to its vomit, so a fool repeats his foolishness. Chitsiru chimene chimabwerezabwereza uchitsiru wake chili ngati galu amene amabwerera ku masanzi ake.
12 Do you see someone wise in his own eyes? There is more hope for a fool than for him. Munthu wa uchitsiru aliko bwino popeza pali chiyembekezo kuposana ndi munthu amene amadziyesa yekha kuti ndi wanzeru.
13 The lazy person says, "There is a lion in the road! A lion in the streets!" Munthu waulesi amati, “Mu msewu muli mkango, mkango woopsa ukuyendayenda mʼmisewu!”
14 As a door turns on its hinges, so the lazy person turns on his bed. Monga chitseko chimapita uku ndi uku pa zolumikizira zake, momwemonso munthu waulesi amangotembenukatembenuka pa bedi lake.
15 The lazy person buries his hand in the dish; it wearies him to bring it back to his mouth. Munthu waulesi akapisa dzanja lake mu mʼbale; zimamutopetsa kuti alifikitse pakamwa pake.
16 The lazy person is wiser in his own eyes than seven who answer wisely. Munthu waulesi amadziyesa yekha wanzeru kuposa anthu asanu ndi awiri amene amayankha mochenjera.
17 Like grabbing a dog by the ears is a passerby who meddles in a quarrel not his own. Munthu wongolowera mikangano imene si yake ali ngati munthu wogwira makutu a galu wongodziyendera.
18 Like a madman shooting firebrands, arrows, and death, Monga munthu wamisala amene akuponya sakali zamoto kapena mivi yoopsa,
19 so is the one who deceives his neighbor and says, "I was only joking!" ndi momwe alili munthu wonamiza mnzake, amene amati, “Ndimangoseka chabe!”
20 Without wood a fire goes out, and without a gossip a quarrel dies down. Pakasowa nkhuni, moto umazima; chomwechonso pakasowa anthu amiseche mkangano umatha.
21 As charcoal to embers and wood to fire, so a quarrelsome person kindles strife. Monga alili makala pa moto wonyeka kapena mmene zimachitira nkhuni pa moto, ndi mmene alili munthu wolongolola poyambitsa mikangano.
22 The words of a gossip are like choice morsels; they sink down into the inmost parts. Mawu a munthu wamiseche ali ngati chakudya chokoma; chimene chimatsikira mʼmimba mwa munthu.
23 Like a glaze covering an earthen pot are smooth lips with an evil heart. Monga mmene chiziro chimakutira chiwiya chadothi ndi mmene mawu oshashalika amabisira mtima woyipa.
24 An enemy disguises himself with his lips, but in his heart he harbors deceit. Munthu wachidani amayankhula zabwino pamene mu mtima mwake muli chinyengo.
25 When he speaks graciously, do not believe him, for seven abominations fill his heart. Ngakhale wotereyu mawu ake ali okoma, koma usamukhulupirire, pakuti mu mtima mwake mwadzaza zonyansa.
26 Though his hatred is hidden by deceit, his wickedness will be exposed in the assembly. Ngakhale amabisa chidani mochenjera, koma kuyipa kwakeko kudzaonekera poyera pa gulu la anthu.
27 Whoever digs a pit will fall into it, and a stone rolls back on the one who rolls it. Ngati munthu akumba dzenje, adzagweramo yekha; ngati munthu agubuduza mwala, udzamupsinja iye mwini.
28 A lying tongue hates those it crushes, and a flattering mouth works ruin. Munthu wonama amadana ndi amene anawapweteka, ndipo pakamwa poshashalika pamabweretsa chiwonongeko.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]