Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 27 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Do not boast about tomorrow, for you do not know what a day may bring. Usamanyadire za mawa, pakuti sudziwa zimene zidzachitike pa tsikulo.
2 Let someone else praise you, and not your own mouth; a stranger, and not your own lips. Munthu wina akutamande, koma osati wekha; mlendo akakutamanda, ndiponi koma osati ndi pakamwa pako.
3 A stone is heavy and the sand a burden, but a fool's provocation is heavier than both. Mwala ndi wolemera ndipo mchenganso ndi wolemera kwambiri, koma makani a chitsiru ndi oposa zonsezo kulemera kwake.
4 Wrath is cruel and anger is overwhelming, but who can stand before jealousy? Mkwiyo umadzetsa nkhanza ndipo kupsa mtima kumachititsa zoopsa. Koma nsanje imachita zoopsa zopambana.
5 Open rebuke is better than love that stays hidden. Kudzudzula munthu poyera nʼkwabwino kuposa chikondi chobisika.
6 A friend's wounds are faithful, but an enemy's kisses are deceitful. Munthu amene amakukonda ngakhale akupweteke zili bwino, koma mdani wako amakupsompsona mwachinyengo.
7 A well-fed person tramples honeycomb, but to the hungry even what is bitter tastes sweet. Iye amene wakhuta amayipidwa ndi chisa cha uchi, koma kwa munthu wanjala ngakhale chimene chili chowawa chimamukomera.
8 A man who strays from his home is like a bird that strays from its nest. Munthu amene wasochera ku nyumba kwake, ali monga mbalame imene yasochera pa chisa chake.
9 Oil and incense gladden the heart, and the sweetness of a friend comes from heartfelt counsel. Mafuta ndi zonunkhira zimasangalatsa mtima, ndipo kukoma mtima kwa bwenzi kwagona pa malangizo ake.
10 Do not forsake your friend or your father's friend, and do not go to your brother's house when disaster strikes; better a neighbor nearby than a brother far off. Usasiye bwenzi lako ndiponso bwenzi la abambo ako, ndipo usapite ku nyumba ya mʼbale wako pamene wakumana ndi mavuto; mnzako wokhala naye pafupi amaposa mʼbale wako wokhala kutali.
11 Be wise, my son, and make my heart glad, so that I can answer anyone who taunts me. Mwana wanga, khala wanzeru, ndipo ukondweretse mtima wanga; pamenepo ine ndidzatha kuyankha aliyense amene amandinyoza.
12 The prudent sees danger and takes cover, but the simple keep going and pay the price. Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala, koma munthu wopusa amangopitirira ndipo amakumana ndi mavuto.
13 Take the garment of one who puts up security for a stranger; hold it as collateral when he does so for a foreign woman. Utenge chovala cha munthu amene waperekera mlendo chikole; ngati chigwiriro chifukwa waperekera chikole mlendo wosadziwika.
14 Whoever blesses his neighbor with a loud voice early in the morning, it will be taken as a curse. Ngati munthu apatsa mnzake moni mofuwula mmamawa kwambiri, anthu adzamuyesa kuti akutemberera.
15 A quarrelsome wife is like a constant dripping on a rainy day. Mkazi wolongolola ali ngati mvula yamvumbi.
16 Restraining her is like restraining the wind, or grasping oil with the right hand. Kumuletsa mkazi wotereyu zimenezi zili ngati kuletsa mphepo kapena kufumbata mafuta mʼdzanja.
17 Iron sharpens iron, and one person sharpens another. Chitsulo chimanoledwa ndi chitsulo chinzake, chomwechonso munthu amanoledwa ndi munthu mnzake.
18 Whoever tends a fig tree will eat its fruit, and whoever guards his master will be honored. Amene amasamalira mtengo wamkuyu adzadya zipatso zake, ndipo iye amene amasamalira mbuye wake adzalandira ulemu.
19 As water reflects the face, so the heart reflects the person. Monga momwe nkhope imaonekera mʼmadzi, chomwechonso mtima wa munthu umadziwika ndi ntchito zake.
20 The grave and Destruction are never satisfied, and a person's eyes are never satisfied. Manda sakhuta, nawonso maso a munthu sakhuta.
21 The crucible is for silver and the furnace for gold, and a person is tested by the praise he receives. Siliva amasungunulira mu uvuni ndipo golide mʼngʼanjo, chomwechonso munthu amadziwika ndi zomwe akudzitamandira nazo.
22 Though you grind a fool in a mortar with a pestle, along with the grain, his foolishness will not leave him. Ngakhale utakonola chitsiru mu mtondo ndi musi ngati chimanga, uchitsiru wakewo sudzachoka.
23 Know well the condition of your flocks, and give careful attention to your herds. Uzidziwe bwino nkhosa zako momwe zilili. Kodi usamalire bwino ziweto zako?
24 For riches do not last forever, nor does a crown endure to every generation. Paja chuma sichikhala mpaka muyaya, ndipo ufumu sukhala mpaka mibado yonse.
25 When the grass is gone and the new growth appears and the mountain herbs are gathered, Pamene udzu watha, msipu nʼkumera; ndipo atatuta udzu wa ku mapiri,
26 the lambs will provide your clothing, and the goats will provide the price of a field; ana ankhosa adzakupatsani chovala ndipo pogulitsa mbuzi mudzapeza ndalama yogulira munda.
27 and there will be enough goats' milk for your food, for the food of your household and to sustain your servant girls. Mudzakhala ndi mkaka wambuzi wambiri kuti muzidya inuyo ndi banja lanu ndi kudyetsa antchito anu aakazi.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]