Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 28 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 The wicked flee when no one pursues, but the righteous are as bold as a lion. Munthu woyipa amathawa ngakhale palibe wina womuthamangitsa, koma wolungama ndi wolimba mtima ngati mkango.
2 When a land rebels, it has many rulers, but with a man of understanding and knowledge, it stays stable. Pamene mʼdziko muli kuwukirana, dzikolo limakhala ndi olamulira ambiri, koma anthu omvetsa ndi odziwa zinthu bwino ndiwo angakhazikitse bata mʼdzikolo nthawi yayitali.
3 A poor man who oppresses the helpless is like a driving rain that leaves no food. Munthu wosauka amene amapondereza osauka anzake ali ngati mvula yamkuntho imene imawononga mbewu mʼmunda.
4 Those who forsake the law praise the wicked, but those who keep the law strive against them. Amene amakana malamulo amatamanda anthu oyipa, koma amene amasunga malamulo amatsutsana nawo.
5 Evil people do not understand justice, but those who seek our Father understand it fully. Anthu oyipa samvetsa za chiweruzo cholungama, koma amene amafuna kuchita zimene Yehova afuna amachimvetsetsa bwino.
6 Better is a poor man who walks with integrity than a rich man crooked in his ways. Munthu wosauka wa makhalidwe abwino aposa munthu wolemera wa makhalidwe okhotakhota.
7 Whoever keeps the law is a son with understanding, but a companion of gluttons shames his father. Amene amasunga malamulo ndi mwana wozindikira zinthu, koma amene amayenda ndi anthu adyera amachititsa manyazi abambo ake.
8 Whoever multiplies his wealth by interest and unjust gain gathers it for one who is generous to the poor. Amene amachulukitsa chuma chake polandira chiwongoladzanja chochuluka amakundikira chumacho anthu ena, amene adzachitira chifundo anthu osauka.
9 If anyone refuses to listen to the law, even his prayer is detestable. Wokana kumvera malamulo ngakhale pemphero lake lomwe limamunyansa Yehova.
10 Whoever leads the upright astray down an evil path will fall into his own pit, but the blameless will inherit good things. Amene amatsogolera anthu olungama kuti ayende mʼnjira yoyipa adzagwera mu msampha wake womwe, koma anthu opanda cholakwa adzalandira cholowa chabwino.
11 A rich man is wise in his own eyes, but a poor man with understanding sees right through him. Munthu wolemera amadziyesa kuti ndi wanzeru, koma munthu wosauka amene ali ndi nzeru zodziwa zinthu amamutulukira.
12 When the righteous triumph, there is great glory, but when the wicked rise, people go into hiding. Pamene olungama apambana pamakhala chikondwerero chachikulu; koma pamene anthu oyipa apatsidwa ulamuliro, anthu amabisala.
13 Whoever conceals his sins will not prosper, but whoever confesses and turns from them will find mercy. Wobisa machimo ake sadzaona mwayi, koma aliyense amene awulula ndi kuleka machimowo, adzalandira chifundo.
14 Blessed is the one who always remains reverent, but whoever hardens his heart will fall into calamity. Ndi wodala munthu amene amaopa Yehova nthawi zonse, koma amene aumitsa mtima wake adzagwa mʼmavuto.
15 Like a roaring lion or a charging bear is a wicked ruler over a helpless people. Ngati mkango wobuma kapena chimbalangondo cholusa ndi mmenenso amakhalira munthu woyipa akamalamulira anthu osauka.
16 A ruler who lacks understanding is a cruel oppressor, but whoever hates unjust gain will prolong his days. Wolamulira amene samvetsa zinthu ndiye amakhala wankhanza koma amene amadana ndi phindu lopeza mwachinyengo adzakhala ndi moyo wautali.
17 A man weighed down by the guilt of bloodshed will be a fugitive until death; let no one support him. Munthu amene wapalamula mlandu wopha munthu adzakhala wothawathawa mpaka imfa yake; wina aliyense asamuthandize.
18 Whoever walks in integrity will be kept safe, but whoever is crooked in his ways will suddenly fall. Amene amayenda mokhulupirika adzapulumutsidwa koma amene njira zake ndi zokhotakhota adzagwa mʼdzenje.
19 Whoever works his land will have plenty of bread, but whoever chases empty pursuits will have plenty of poverty. Amene amalima mʼmunda mwake adzakhala ndi chakudya chochuluka, koma amene amangosewera adzakhala mʼmphawi.
20 A faithful man will abound with blessings, but whoever rushes to get rich will not go unpunished. Munthu wokhulupirika adzadalitsika kwambiri, koma wofuna kulemera mofulumira adzalangidwa.
21 Showing partiality is not good, yet for a piece of bread a man will do wrong. Kukondera si kwabwino, ena amachita zolakwazo chifukwa cha kachidutswa ka buledi.
22 A stingy man rushes after wealth and does not know that poverty will overtake him. Munthu wowumira amafunitsitsa kulemera koma sazindikira kuti umphawi udzamugwera.
23 Whoever rebukes a man will in the end find more favor than one who flatters with his tongue. Amene amadzudzula mnzake potsiriza pake mnzakeyo adzamukonda kwambiri, kupambana amene amanena mawu oshashalika.
24 Whoever robs his father or mother and says, "It is no sin," is a companion to one who destroys. Amene amabera abambo ake kapena amayi ake namanena kuti “kumeneko sikulakwa,” ndi mnzake wa munthu amene amasakaza.
25 A greedy man stirs up strife, but whoever trusts in our Father will be enriched. Munthu wadyera amayambitsa mikangano, koma amene amadalira Yehova adzalemera.
26 Whoever trusts in his own heart is a fool, but whoever walks in wisdom will be kept safe. Amene amadzidalira yekha ndi chitsiru, koma amene amatsata nzeru za ena adzapulumuka.
27 Whoever gives to the poor will lack nothing, but whoever closes his eyes to them will receive many curses. Amene amapereka kwa osauka sadzasowa kanthu, koma amene amatsinzina maso ake adzatembereredwa kwambiri.
28 When the wicked rise, people go into hiding, but when they perish, the righteous flourish. Pamene anthu oyipa apatsidwa ulamuliro anthu amabisala, koma anthu oyipa akawonongeka olungama amapeza bwino.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]