Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 29 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Whoever is often corrected yet refuses to listen will suddenly be broken beyond healing. Munthu amene amawumitsabe khosi lake atadzudzulidwa kwambiri, adzawonongeka mwadzidzidzi popanda chomuchiritsa.
2 When the righteous flourish, the people rejoice, but when the wicked rule, the people groan. Anthu olungama akamalamulira mʼdziko anthu amakondwa, koma ngati dziko lilamulidwa ndi anthu oyipa mtima anthu amadandaula.
3 A man who loves wisdom brings joy to his father, but a companion of prostitutes squanders his wealth. Munthu amene amakonda nzeru amasangalatsa abambo ake, koma woyenda ndi akazi achiwerewere amasakaza chuma chake.
4 By justice a king gives a land stability, but one who is greedy for bribes tears it down. Mfumu imalimbitsa dziko poweruza mwachilungamo, koma mfumu imene imawumiriza anthu kuti ayipatse mphatso imawononga dziko.
5 A man who flatters his neighbor spreads a net for his feet. Munthu woshashalika mnzake, akudziyalira ukonde mapazi ake.
6 An evil man is snared by his own sin, but the righteous sing and rejoice. Munthu woyipa amakodwa ndi machimo ake, koma wochita chilungamo amayimba lokoma.
7 The righteous care about justice for the poor, but the wicked have no such understanding. Munthu wolungama amasamalira anthu osauka, koma woyipa salabadira zimenezi.
8 Mockers set a city ablaze, but the wise calm the anger. Anthu onyoza atha kuwutsa ziwawa mu mzinda, koma anthu anzeru amaletsa ukali.
9 When a wise man goes to court with a fool, the fool rages and scoffs, and there is no peace. Ngati munthu wanzeru atsutsana ndi chitsiru, chitsirucho chimachita phokoso ndi kumangoseka ndipo sipakhala mtendere.
10 The bloodthirsty hate the blameless and seek to kill the upright. Anthu okhetsa magazi amadana ndi munthu wangwiro koma anthu olungama amasamalira moyo wake.
11 A fool vents all his anger, but a wise man holds it back and keeps himself calm. Munthu wopusa amaonetsa mkwiyo wake, koma munthu wanzeru amadzigwira.
12 If a ruler listens to lies, all his officials become wicked. Ngati wolamulira amvera zabodza, akuluakulu ake onse adzakhala oyipa.
13 The poor man and the oppressor have this in common: our Father gives sight to the eyes of both. Munthu wosauka ndi munthu wopondereza anzake amafanana pa kuti: Yehova ndiye anawapatsa maso onsewa.
14 If a king judges the poor with fairness, his throne will be established forever. Ngati mfumu iweruza osauka moyenera, mpando wake waufumu udzakhazikika nthawi zonse.
15 The rod and a word of correction give wisdom, but a child left to himself brings shame to his mother. Ndodo ndi chidzudzulo zimapatsa nzeru koma mwana womulekerera amachititsa amayi ake manyazi.
16 When the wicked flourish, wrongdoing flourishes, but the righteous will see the wicked's downfall. Oyipa akamalamulira zoyipa zimachuluka, koma anthu olungama adzaona kugwa kwa anthu oyipawo.
17 Discipline your son, and he will give you peace; he will bring delight to your heart. Umulange mwana wako ndipo adzakupatsa mtendere ndi kusangalatsa mtima wako.
18 Where there is no revelation, the people run wild, but blessed is the one who keeps the law. Ngati uthenga wochokera kwa Yehova supezeka anthu amangochita zofuna zawo; koma wodala ndi amene amasunga malamulo.
19 A servant cannot be corrected by words alone; though he understands, he will not obey. Munthu wantchito sangalangizidwe ndi mawu okha basi; ngakhale awamvetse mawuwo sadzatha kuchitapo kanthu.
20 Do you see a man who is hasty with his words? There is more hope for a fool than for him. Ngakhale munthu wa uchitsiru nʼkuti ndiponi popeza chikhulupiriro chilipo kuposa munthu wodziyesa yekha kuti ndi wanzeru poyankhula.
21 Pamper a servant from childhood, and in the end he will become like an heir. Ngati munthu asasatitsa wantchito wake kuyambira ali mwana, potsirizira adzapeza kuti wantchitoyo wasanduka mlowachuma wake.
22 An angry man stirs up strife, and a hot-tempered man commits many sins. Munthu wamkwiyo amayambitsa mikangano, ndipo munthu waukali amachita zolakwa zambiri.
23 A man's pride brings him low, but a humble spirit gains honor. Kunyada kwa munthu kudzamutsitsa, koma munthu wodzichepetsa amalandira ulemu.
24 An accomplice of a thief is his own enemy; he hears the curse but says nothing. Woyenda ndi munthu wakuba ndi mdani wa moyo wake womwe; amalumbira koma osawulula kanthu.
25 Fear of man lays a snare, but whoever trusts in our Father is kept safe. Kuopa munthu kudzakhala ngati msampha, koma aliyense amene amadalira Yehova adzatetezedwa.
26 Many seek a ruler's favor, but justice for a person comes from our Father. Anthu ambiri amafunitsitsa kuti wolamulira awakomere mtima, koma munthu amaweruzidwa mwachilungamo ndi thandizo la Yehova basi.
27 An unjust man is detestable to the righteous, and an upright person is detestable to the wicked. Anthu olungama amanyansidwa ndi anthu achinyengo; koma anthu oyipa amanyansidwa ndi anthu a mtima wowongoka.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]