Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 30 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 The words of Agur son of Jakeh—the oracle. The man declares: I am weary, O my Father; I am weary, O my Father, and worn out. Nawa mawu a Aguri mwana wa Yake wa ku Masa: Munthuyo anati kwa Itieli, “Inu Mulungu, ine ndatopa. Inu Mulungu, ine ndatopa. Ndalefukiratu.
2 Surely I am too brutish to be a man; I do not have the understanding of a man. “Ine ndine munthu wopusa kuposa anthu onse; ndilibe nzeru zomvetsa zinthu zonga za munthu.
3 I have not learned wisdom, nor do I have knowledge of the Holy One. Sindinaphunzire nzeru, ndipo Woyerayo sindimudziwa.
4 Who has ascended to heaven and come down? Who has gathered the wind in the hollow of his hands? Who has wrapped the waters in a garment? Who has established all the ends of the earth? What is his name, and what is his son's name? Surely you know! Kodi ndani anakwera kumwamba ndi kutsikako? Ndani anafumbatapo mphepo mʼmanja mwake? Ndani anamanga madzi mʼchovala chake? Ndani anakhazikitsa mathero onse a dziko lapansi? Dzina lake ndani? Ndiwuze ngati ukudziwa! Ndipo mwana wake dzina lake ndani?
5 Every word of our Father proves true; he is a shield to those who take refuge in him. “Mawu ali wonse a Mulungu ndi opanda cholakwika; Iye ndi chishango kwa amene amathawira kwa Iye.
6 Do not add to his words, or he will rebuke you and prove you a liar. Usawonjezepo kanthu pa mawu ake, kuopa kuti Iye angadzakudzudzule ndi kukupeza kuti ndiwe wabodza.”
7 Two things I ask of you; do not withhold them from me before I die: “Inu Yehova, ndikukupemphani zinthu ziwiri musandimane zimenezo ndisanafe:
8 Keep falsehood and lies far from me; give me neither poverty nor riches; feed me only the bread that is my portion, Choyamba, mundichotsere kutali nane mabodza ndi chinyengo. Chachiwiri, ndisakhale mʼmphawi kapena munthu wachuma. Koma muzindidyetsa chakudya chondikwanira tsiku ndi tsiku
9 for if I am full, I may deny you and say, "Who is God?" or if I am poor, I may steal and profane the name of my God. kuopa kuti ndikakhuta kwambiri ndingayambe kukukanani, nʼkumanena kuti, ‘Yehova ndiye yaninso?’ Kuopanso kuti ndikakhala wosauka ndingayambe kuba, potero nʼkuyipitsa dzina la Mulungu wanga.”
10 Do not slander a servant to his master, or he will curse you and you will be found guilty. “Usamusinjirire wantchito kwa mbuye wake kuopa kuti angakutemberere ndipo iweyo nʼkupezeka wolakwa.”
11 There is a generation that curses its father and does not bless its mother. “Alipo ena amene amatemberera abambo awo, ndipo sadalitsa amayi awo.
12 There is a generation clean in its own eyes yet not washed of its filth. Pali ena amene amadziyesa okha oyera mtima komatu sanachotse zoyipa zawo.
13 There is a generation—how proud its eyes, how scornful its glances! Pali ena ndi odzitukumula kwambiri, amene amakweza zikope modzitukumula.
14 There is a generation whose teeth are swords, whose fangs are knives, to devour the poor from the earth and the needy from among mankind. Pali ena amene mano awo ali ngati malupanga ndipo zibwano zawo zili ngati mipeni moti amadya amphawi ndi kuwachotsa pa dziko lapansi. Amachotsanso anthu osauka pakati pa anzawo.”
15 The leech has two daughters: "Give" and "Give." Three things are never satisfied; four never say, "Enough": “Msundu uli ndi ana aakazi awiri iwo amalira kuti, ‘Tipatseni! Tipatseni!’ ” “Pali zinthu zitatu zimene sizikhuta, zinthu zinayi zimene sizinena kuti, ‘Takhuta!’
16 The grave, the barren womb, the land never satisfied with water, and the fire that never says, "Enough." Manda, mkazi wosabala, nthaka yosakhuta madzi ndiponso moto womangoyakirayakira!”
17 The eye that mocks a father and scorns to obey a mother—the ravens of the valley will pluck it out, and the young vultures will eat it. Aliyense amene amanyoza abambo ake, ndi kunyozera kumvera amayi ake, makwangwala a ku chigwa adzamukolowola maso ndipo mphungu zidzadya mnofu wake.
18 Three things are too wonderful for me; four I do not understand: Pali zinthu zitatu zimene zimandidabwitsa, zinthu zinayi zimene ine sindizimvetsetsa.
19 the way of an eagle in the sky, the way of a serpent on a rock, the way of a ship in the heart of the sea, and the way of a man with a young woman. Ndipo ndi izi: mmene chiwulukira chiwombankhanga mlengalenga; mmene iyendera njoka pa thanthwe; mmene chiyendera chombo pa nyanja; ndiponso mmene mwamuna achitira akakhala ndi namwali.
20 This is the way of an adulteress: she eats and wipes her mouth and says, "I have done no wrong." Umu ndi mʼmene mkazi amachitira atachita chigololo: Atatha kudya ndi kupukuta pakamwa pake iye amanena kuti “Sindinachite kalikonse kolakwa.”
21 Under three things the earth trembles; under four it cannot bear up: Pali zinthu zitatu zimene zimanjenjemeretsa dziko lapansi, pali zinthu zinayi zimene dziko lapansi silingathe kuzipirira:
22 a servant when he becomes king, and a fool when he is filled with food; Kapolo amene wasanduka mfumu, chitsiru chimene chakhuta,
23 an unloved woman when she finally marries, and a servant girl when she displaces her mistress. mkazi wonyozeka akakwatiwa ndiponso wantchito wamkazi akalanda mwamuna wa mbuye wake.
24 Four things on earth are small, yet they are exceedingly wise: Pali zinthu zinayi zingʼonozingʼono pa dziko lapansi, komatu ndi zochenjera kwambiri:
25 the ants are a people not strong, yet they store up their food in the summer; Nyerere zili ngati anthu opanda mphamvu, komatu zimasungiratu chakudya chake nthawi ya chilimwe;
26 the rock badgers are a people not mighty, yet they make their homes in the cliffs; mbira zili ngati anthu opanda mphamvu komatu zimakonza pokhalapo pawo mʼmiyala;
27 the locusts have no king, yet all of them advance in ranks; dzombe lilibe mfumu, komatu lonse limakhala mʼmagulumagulu poyenda.
28 the lizard you can catch in your hands, yet it is found in kings' palaces. Buluzi ungathe kumugwira mʼmanja komatu amapezeka mʼnyumba za mafumu.
29 Three things are stately in their stride; four are stately in their walk: “Pali zinthu zitatu zimene zimayenda chinyachinya, pali zinthu zinayi zimene zimayenda monyadira:
30 the lion, mightiest among beasts, which turns back before nothing; Mkango umene uli wamphamvu kuposa nyama zonse, ndipo suthawa kanthu kalikonse.
31 the strutting rooster, the male goat, and a king whose army is with him. Tambala woyenda chinyachinya, mbuzi yayimuna, ndiponso mfumu yoyenda pakati pa anthu ake.
32 If you have been foolish, exalting yourself, or if you have schemed evil, put your hand over your mouth. “Ngati wakhala ukupusa ndi kumadzikweza wekha, kapena ngati wakhala ukukonzekera zoyipa, ndiye khala kaye chete, uganizire bwino!
33 For pressing milk produces curds, pressing the nose produces blood, and pressing anger produces strife. Paja pakutha mkaka mafuta amapangidwa, ndipo ukapsinya mphuno, magazi amatuluka, ndipo mikangano imakhalapo ukalimbikira kukwiya.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]