Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Proverbs 31 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 The words of King Lemuel—an oracle his mother taught him: Nawa mawu a mfumu Lemueli wa ku Massa amene anamuphunzitsa amayi ake:
2 What, my son? What, son of my womb? What, son of my vows? Nʼchiyani mwana wanga? Nʼchiyani mwana wa mʼmimba mwanga? Nʼchiyani iwe mwana wanga amene ndinachita kupempha ndi malumbiro?
3 Do not give your strength to women, or your ways to those who destroy kings. Usapereke mphamvu yako kwa akazi. Usamayenda nawo amenewa popeza amawononga ngakhale mafumu.
4 It is not for kings, Lemuel—not for kings to drink wine, or for rulers to crave strong drink. Iwe Lemueli si choyenera kwa mafumu, mafumu sayenera kumwa vinyo. Olamulira asamalakalake chakumwa choledzeretsa
5 For if they drink, they will forget what is decreed and pervert the rights of all the oppressed. kuopa kuti akamwa adzayiwala malamulo a dziko, nayamba kukhotetsa zinthu zoyenera anthu osauka.
6 Give strong drink to one who is perishing, and wine to those in bitter distress. Perekani chakumwa choledzeretsa kwa amene ali pafupi kufa, vinyo kwa amene ali pa mavuto woopsa;
7 Let them drink and forget their poverty, and remember their misery no more. amwe kuti ayiwale umphawi wawo asakumbukirenso kuvutika kwawo.
8 Open your mouth for the voiceless, for the rights of all who are left destitute. Yankhula mʼmalo mwa amene sangathe kudziyankhulira okha. Uwayankhulire anthu onse osiyidwa pa zonse zowayenera.
9 Open your mouth, judge righteously, and defend the rights of the poor and needy. Yankhula ndi kuweruza mwachilungamo. Uwateteze amphawi ndi osauka.
10 A woman of valor—who can find her? She is far more precious than jewels. Kodi mkazi wangwiro angathe kumupeza ndani? Ndi wokwera mtengo kuposa miyala yamtengowapatali.
11 The heart of her husband trusts in her, and he will lack nothing of value. Mtima wa mwamuna wake umamukhulupirira ndipo mwamunayo sasowa phindu.
12 She does him good and not harm, all the days of her life. Masiku onse a moyo wake mkaziyo amachitira mwamuna wake zabwino zokhazokha osati zoyipa.
13 She seeks out wool and flax, and works with willing hands. Iye amafunafuna ubweya ndi thonje; amagwira ntchito ndi manja ake mwaufulu.
14 She is like the merchant ships, bringing her food from afar. Iye ali ngati sitima zapamadzi za anthu amalonda, amakatenga chakudya chake kutali.
15 She rises while it is still night, provides food for her household, and portions for her servant girls. Iye amadzuka kusanache kwenikweni; ndi kuyamba kukonzera a pa banja pake chakudya ndi kuwagawira ntchito atsikana ake antchito.
16 She considers a field and buys it; from the fruit of her hands she plants a vineyard. Iye amalingalira za munda ndi kuwugula; ndi ndalama zimene wazipeza amalima munda wamphesa.
17 She wraps herself in strength and makes her arms strong. Iye amavala zilimbe nagwira ntchito mwamphamvu ndi manja ake.
18 She perceives that her trading is profitable; her lamp does not go out at night. Iye amaona kuti malonda ake ndi aphindu, choncho nyale yake sizima usiku wonse.
19 She puts her hands to the spinning staff, and her hands grasp the spindle. Iye amadzilukira thonje ndipo yekha amagwira chowombera nsalu.
20 She opens her hand to the poor and reaches out her hands to the needy. Iye amachitira chifundo anthu osauka ndipo amapereka chithandizo kwa anthu osowa.
21 She has no fear for her household when it snows, for all her household are clothed in scarlet. Iye saopa kuti banja lake lifa ndi kuzizira pa nyengo yachisanu; pakuti onse amakhala atavala zovala zofunda.
22 She makes coverings for herself; her clothing is fine linen and purple. Iye amadzipangira yekha zoyala pa bedi pake; amavala zovala zabafuta ndi zapepo.
23 Her husband is known in the gates, when he sits among the elders of the land. Mwamuna wake ndi wodziwika pa chipata cha mzinda, ndipo amakhala pakati pa akuluakulu a mʼdzikomo.
24 She makes linen garments and sells them, and supplies sashes to the merchants. Iye amasoka nsalu zabafuta nazigulitsa; amaperekanso mipango kwa anthu amalonda.
25 Strength and dignity are her clothing, and she laughs at the days to come. Mphamvu ndi ulemu zimakhala ngati chovala chake; ndipo amaseka osaopa zamʼtsogolo.
26 She opens her mouth with wisdom, and faithful instruction is on her tongue. Iye amayankhula mwanzeru, amaphunzitsa anthu mwachikondi.
27 She watches over the ways of her household and does not eat the bread of idleness. Iye amayangʼanira makhalidwe a anthu a pa banja lake ndipo sachita ulesi ndi pangʼono pomwe.
28 Her children rise up and call her blessed; her husband also, and he praises her: Ana ake amamunyadira ndipo amamutcha kuti wodala; ndipo mwamuna wake, amamuyamikira nʼkumati,
29 "Many daughters have done valiantly, but you surpass them all." “Pali akazi ambiri amene achita zinthu zopambana koma iwe umawaposa onsewa.”
30 Charm is deceptive and beauty is fleeting, but a woman who reveres our Father—she will be praised. Nkhope yachikoka ndi yonyenga, ndipo kukongola nʼkosakhalitsa; koma mkazi amene amaopa Yehova ayenera kutamandidwa.
31 Give her the fruit of her hands, and let her works praise her in the gates. Mupatseni mphotho chifukwa cha zimene iye wachita ndipo ntchito zake zimutamande ku mabwalo.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]