Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Ecclesiastes 1 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 The words of the Teacher, son of David, king in Jerusalem. Mawu a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya ku Yerusalemu:
2 "Utterly fleeting," says the Teacher, "utterly fleeting! Everything is fleeting." “Zopandapake! Zopandapake!” atero Mlaliki. “Zopandapake kotheratu! Zopandapake.”
3 What does a person gain from all the labor at which they toil under the sun? Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zake zonse zimene amasautsidwa nazo pansi pano?
4 A generation goes, and a generation comes, but the earth remains forever. Mibado imabwera ndipo mibado imapita, koma dziko lapansi limakhalapobe nthawi zonse.
5 The sun rises and the sun sets, and hurries back to the place where it rises. Dzuwa limatuluka ndipo dzuwa limalowa ndipo limapita mwamsanga kumene limatulukira.
6 The wind blows to the south and turns to the north; round and round it goes, ever returning on its circuits. Mphepo imawombera cha kummwera ndi kukhotera cha kumpoto; imawomba mozungulirazungulira, kumangobwererabwerera komwe yachokera.
7 All the streams run to the sea, yet the sea is never full; the streams return to their source and flow again. Mitsinje yonse imakathira ku nyanja, koma nyanjayo sidzaza; kumene madziwo amachokera, amabwereranso komweko.
8 All things are wearisome, more than anyone can express; the eye is not satisfied with seeing, nor the ear filled with hearing. Zinthu zonse ndi zotopetsa, kutopetsa kwake ndi kosaneneka. Maso satopa ndi kuona kapena khutu kukwaniritsidwa ndi kumva.
9 What has been is what will be, and what has been done is what will be done; there is nothing new under the sun. Zomwe zinalipo kale zidzakhalaponso, zomwe zinachitika kale zidzachitikanso. Ndiye kuti chatsopano palibiretu pansi pano.
10 Is there anything anyone can point to and say, "Look, this is new"? It was already here, in the ages before us. Kodi chilipo chinthu chimene wina anganene kuti, “Taona! Ichi ndiye chatsopano?” Chinalipo kale, kalekale; chinalipo ife kulibe.
11 There is no remembrance of those who came before, and even those yet to come will not be remembered by those who follow them. Anthu akale sakumbukiridwa, ngakhale amene adzabwera mʼtsogolomu sadzakumbukiridwa ndi iwo amene adzabwere pambuyo pawo.
12 I, the Teacher, was king over Israel in Jerusalem. Ine, Mlalikine, ndinali mfumu ya Israeli mu Yerusalemu.
13 I gave my heart to seek and explore by wisdom all that is done under heaven—a miserable task God has given mankind to struggle with. Ndinayika mtima wanga pophunzira ndi kufunafuna mwa nzeru zinthu zonse zimene zimachitika pansi pa thambo. Ndi ntchito yolemetsa ndithu imene Mulungu anayipereka kwa anthu!
14 I saw all the deeds done under the sun, and look—it is all fleeting, a chasing after wind. Ine ndaona zinthu zonse zochitika pansi pano; zinthu zonsezo ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.
15 What is crooked cannot be made straight, and what is lacking cannot be counted. Chinthu chokhota sichingathe kuwongoledwa; chimene palibe sichingathe kuwerengedwa.
16 I told myself, "Look, I have grown great and gained more wisdom than all who ruled Jerusalem before me; my heart has seen much wisdom and knowledge." Ine ndinaganiza mu mtima mwanga, “Taona, ine ndakula ndi kukhala wa nzeru zochuluka kupambana aliyense amene analamulirapo Yerusalemu ndisanabadwe; ndaphunzira nzeru zochuluka ndi luntha.”
17 I set my mind to know wisdom, and madness and foolishness; I learned this too is a chasing after the wind. Ndipo ndinadzipereka kuti ndithe kumvetsa kuti nzeru nʼchiyani, misala nʼchiyani, uchitsiru nʼchiyani, koma ndinazindikira ichi, kuti kuteronso nʼkungodzivuta chabe.
18 For with much wisdom comes much grief, and the more knowledge, the more sorrow. Pakuti nzeru zochuluka zimabweretsa chisoni chochulukanso: chidziwitso chochuluka, zowawa zochulukanso.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]