Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Psalms 24 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

Salimo la Davide.

1Dziko lapansi ndi la Yehova ndi zonse zimene zili mʼmenemo,dziko ndi onse amene amakhala mʼmenemo;

2pakuti Iye ndiye anayika maziko ake pa nyanjandi kulikhazika pamwamba pa madzi.

3Ndani angakwere phiri la Yehova?Ndani angathe kuyima pa malo ake opatulika?

4Iye amene ali ndi mʼmanja moyera ndi mtima woyera,amene sapereka moyo wake kwa fanokapena kulumbira mwachinyengo.

5Iyeyo adzalandira madalitso kwa Yehovandipo Mulungu mpulumutsi wake adzagamula kuti alibe mlandu.

6Umenewo ndiwo mʼbado wa amene amafunafuna Yehova;amene amafunafuna nkhope yanu, Inu Mulungu wa Yakobo.Sela

7Tukulani mitu yanu inu zipata;tsekukani, inu zitseko zakalekalenu,kuti Mfumu yaulemerero ilowe.

8Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani?Yehova Wamphamvuzonse,Yehova ndiye wamphamvu pa nkhondo.

9Tukulani mitu yanu, inu zipata;tsekukani, inu zitseko zakalekalenu,kuti Mfumu yaulemerero ilowe.

10Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani?Yehova Wamphamvuzonse,Iye ndiye Mfumu yaulemerero.Sela

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]