Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 56 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 This is what our Father says: Keep justice and do what is right, for my salvation is coming soon, and my righteousness is about to be revealed. Yehova akuti, “Chitani chilungamo ndi zinthu zabwino, chifukwa chipulumutso changa chili pafupi ndipo ndidzakuwombolani posachedwapa.
2 Blessed is the one who does this, the person who holds firmly to it: who keeps the Sabbath without profaning it, and keeps from doing any evil. Ndi wodala munthu amene amachita zimenezi, munthu amene amalimbika kuzichita, amene amasunga Sabata osaliyipitsa, ndipo amadziletsa kuchita zoyipa.”
3 Let not the foreigner who has joined himself to our Father say, "Our Father will surely separate me from his people"; and let not the eunuch say, "I am only a dry tree." Mlendo amene waphatikana ndi Yehova asanene kuti, “Ndithu Yehova wandichotsa pakati pa anthu ake.” Ndipo munthu wofulidwa asanene kuti, “Ine ndine mtengo wowuma basi.”
4 For this is what our Father says: "To the eunuchs who keep my Sabbaths, who choose what pleases me and hold fast to my covenant, Popeza Yehova akuti, “Wofulidwa amene amasunga masabata anga, nachita zokomera Ine ndi kusunga pangano langa,
5 to them I will give within my house and within my walls a memorial and a name better than sons and daughters; I will give them an everlasting name that will not be cut off. ndidzawapatsa dzina ndi mbiri yabwino mʼkati mwa Nyumba yanga ndi makoma ake, kuposa kukhala ndi ana aamuna ndi aakazi. Ndidzawapatsa dzina labwino, losatha ndi losayiwalika.”
6 And the foreigners who join themselves to our Father, to minister to him, to love the name of our Father, and to be his servants—everyone who keeps the Sabbath without profaning it and holds fast to my covenant, Yehova akuti, “Alendo amene amadziphatika kwa Yehova, motero kuti amamutumikira Iye, amakonda dzina la Yehova, amamugwirira ntchito, komanso kusunga Sabata osaliyipitsa ndi kusunga bwino pangano langa,
7 these I will lead up to my holy mountain, and give them joy in my house of prayer; their sacrifices and burnt offerings will be welcome on my altar, since my house will be named a house of prayer for all peoples. amenewa Ine ndidzawafikitsa ku phiri langa lopatulika, ndidzawapatsa chimwemwe mʼnyumba yanga ya mapemphero. Zopereka zawo zopsereza ndi nsembe zawo ndidzazilandira pa guwa langa la nsembe. Paja nyumba yanga idzatchedwa nyumba ya mapemphero ya anthu a mitundu yonse.”
8 This is the declaration of the Sovereign Father, who gathers the outcasts of Israel: I will gather still others to them, besides those already gathered." Ambuye Yehova, amene amasonkhanitsa Aisraeli onse ali ku ukapolo akunena kuti, “Ndidzasonkhanitsano anthu ena kuwonjezera amene anasonkhana kale.”
9 All you beasts of the field, come to devour—all you beasts in the forest. Bwerani, inu zirombo zonse zakuthengo, inu nonse zirombo zamʼnkhalango bwerani mudzadye!
10 Israel's watchmen are blind, all of them; they know nothing. They are all silent dogs that cannot bark, dreaming, lying down, loving to sleep. Atsogoleri onse a Israeli ndi akhungu, onse ndi opanda nzeru; onse ndi agalu opanda mawu, samatha kuwuwa: amagona pansi nʼkumalota amakonda kugona tulo.
11 The dogs have a fierce appetite; they never have enough. They are shepherds with no understanding; they have all turned to their own way, each to his own gain, every one of them. Ali ngati agalu amene ali ndi njala yayikulu; sakhuta konse. Abusa nawonso samvetsa zinthu; onse amachita monga akufunira, aliyense amafunafuna zomupindulitsa iye mwini.
12 "Come," they say, "let me fetch wine; let us drink our fill of strong drink. And tomorrow will be like today, great beyond all measure." Aliyense amafuwulira mnzake kuti, “Bwera, tiye timwe vinyo! Tiyeni timwe mowa mpaka kukhuta! Mawa lidzakhala ngati leroli, kapena kuposa lero lino.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]