Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 57 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 The righteous one perishes, and no one takes it to heart; faithful men are taken away, and no one understands that the righteous are spared from the evil to come. Anthu olungama amafa, ndipo palibe amene amalingalira mu mtima mwake; anthu odzipereka amatengedwa, ndipo palibe amene amamvetsa chifukwa chake. Anthu olungama amatengedwa kuti tsoka lisawagwere.
2 He enters into peace; they rest on their beds—everyone who walks in integrity. Iwo amene amakhala moyo wolungama amafa mwamtendere; amapeza mpumulo pamene agona mu imfa.
3 But you—come here, you children of a sorceress, you offspring of an adulterer and a prostitute! “Bwerani kuno, anthu ochita zoyipa, inu muli ngati zidzukulu za mkazi wachigololo ndi wadama!
4 Who are you mocking? Against whom do you open wide your mouth and stick out your tongue? Are you not children of rebellion, offspring of falsehood, Kodi inu mukuseka yani? Kodi mukumunena ndani ndi kupotoza pakamwa panu? Kodi inu si ana owukira, zidzukulu za anthu abodza?
5 you who burn with lust among the oaks, under every green tree, who slaughter your children in the valleys, under the clefts of the rocks? Inu mumapembedza mafano pamene mumalobodoka ndi zilakolako zanu pakati pa mitengo ya thundu, ndiponso pa tsinde pa mtengo uliwonse wa nthambi zambiri. Mumapereka ana anu ngati nsembe mu zigwa ndiponso mʼmingʼalu ya mʼmatanthwe.
6 Among the smooth stones of the valley is your portion; yes, they are your lot. To them you have poured out a drink offering, you have brought a grain offering. Should I be satisfied with all this? Mafano a pakati pa miyala yosalala ya mu zigwa ndiye chuma chanu. Inde, ndiye gawo lanu. Mumapereka chopereka cha chakumwa kwa mafanowo, ndipo mumaperekanso chopereka cha chakudya. Kodi zimenezi zingandichititse kuti ndikukomereni mtima?
7 On a high and lofty mountain you have set your bed; there too you went up to offer sacrifice. Inu munayiwala bedi lanu pa phiri lalitali ndi looneka kutali. Mumapita kumeneko kukapereka nsembe zanu.
8 Behind the door and the doorpost you have set up your symbol. Deserting me, you uncovered your bed; you went up to it and made it wide. You made a covenant with them; you loved their bed, you gazed on their nakedness. Mʼnyumba mwanu mwayika mafano kuseri kwa zitseko ndiponso pa mphuthu. Mwandisiya Ine, mwavula zovala zanu. Bedi lanu mwalikulitsa ndipo mwakwera ndi zibwenzi zanu, ndiye mwazilipira kuti mugone nazo. Kumene mwakwaniritsa zilakolako zanu zoyipa.
9 You journeyed to the king with oil and heaped up your perfumes; you sent your envoys far away, and sent them down even to the realm of the dead. Mumapita kukapembedza fano la Moleki mutatenga mafuta ndi zonunkhira zochuluka. Munachita kutumiza akazembe anu kutali; inu ngakhale munapita ku manda kwenikweniko!
10 You were wearied by the length of your way, yet you did not say, "It is hopeless." You found renewed strength, and so you did not grow faint. Inu mumatopa ndi maulendo anu, koma simunathe kunena kuti, ‘Nʼzopanda phindu.’ Munapezako kumeneko zokhumba zanu nʼchifukwa chake simunalefuke.
11 Whom did you so dread and fear that you lied, and did not remember me, and gave it no thought? Have I not been silent for so long that you no longer fear me? “Kodi ndani amene mwachita naye mantha ndi kumuopa, kotero kuti mwakhala mukundinamiza, ndipo Ine simundikumbukira nʼkomwe, kapena kuganizirapo mʼmitima yanu za Ine? Kodi mwaleka kundiopa chifukwa choti ndakhala chete nthawi yayitali?
12 I will expose your righteousness and your deeds, but they will not profit you. Koma ndaonetsa poyera ntchito zanu zomwe mumati nʼzolungama, ndi mafano anu kuti nʼzosathandiza.
13 When you cry out, let your collection of idols deliver you! The wind will carry them all off, a breath will take them away. But whoever takes refuge in me will possess the land and inherit my holy mountain. Pamene mufuwula kupempha thandizo, mafano anu amene munasonkhanitsawo ndiyetu akupulumutseni! Mphepo idzanyamula mafano anu onsewo, mpweya chabe udzawulutsa mafanowo. Koma munthu amene amadalira ine adzalandira dziko lokhalamo. Phiri langa lopatulika lidzakhala lakelake.”
14 And it will be said: "Build up, build up, prepare the way! Remove every obstacle from my people's path." Ndipo panamveka mawu akuti, “Undani, undani, konzani msewu! Chotsani zotchinga pa njira yoyendamo anthu anga.”
15 For this is what the high and exalted One says—our Father, who lives forever, whose name is Holy: "I dwell in the high and holy place, and also with the one who is contrite and lowly in spirit, to revive the spirit of the lowly and to revive the heart of the contrite. Pakuti Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthawi zonse, amene dzina lake ndi Woyerayo, akunena kuti, “Ndimakhala pamalo aulemu ndi opatulika, koma ndimakhalanso ndi munthu wodzichepetsa ndi wosweka mtima kuti odzichepetsawo ndiwalimbitse ndi kuwachotsa mantha osweka mtima.
16 For I will not keep fighting forever, nor will I always be angry; for then the spirit would grow faint before me—the very breath of life that I made. Sindidzawatsutsa anthu mpaka muyaya kapena kuwapsera mtima nthawi zonse, popeza kuti ndinalenga anthu anga ndi kuwapatsa mpweya wamoyo.
17 Because of his sinful greed I was angry; I struck him, I hid my face, and I was angry—yet he kept turning away, following the path of his own heart. Ine ndinakwiya kwambiri chifukwa cha tchimo lawo ladyera; ndinawalanga ndi kuwafulatira mokwiya, koma iwo anapitirirabe kuchita ntchito zawo zoyipa.
18 I have seen his ways, but I will heal him; I will lead him and restore comfort to him and to those who mourn for him, Ndaona zochita zawo, komabe ndidzawachiritsa; kuwapumulitsa ndi kuwapatsa mtendere,
19 bringing praise to their lips. Peace, peace to the far and to the near," says our Father, "and I will heal them." anthu olira a mu Israeli adzanditamanda ndi milomo yawo. Anthu amene ali kutali ndi apafupi pomwe ndidzawapatsa mtendere,” “Ndipo ndidzawachiritsa.” Akutero Yehova.
20 But the wicked are like the tossing sea, which cannot be still, whose waters churn up mire and mud. Koma anthu oyipa ali ngati nyanja yowinduka, yosatha kukhala bata, mafunde ake amaponya matope ndi ndere.
21 "There is no peace," says our Father, "for the wicked." “Palibe mtendere kwa oyipa,” akutero Mulungu wanga.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]