Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 55 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 "Listen! All you who are thirsty, come to the water; you without money, come, buy food and eat! Come, buy wine and milk for no price—free of charge. “Bwerani, inu nonse amene muli ndi ludzu, bwerani madzi alipo; ndipo inu amene mulibe ndalama bwerani, mudzagule chakudya kuti mudye! Bwerani mudzagule vinyo ndi mkaka osalipira ndalama, osalipira chilichonse.
2 Why spend money on what is not bread, and your labor on what does not satisfy? Listen carefully to me, and eat what is good, and your soul will delight in the richest food. Chifukwa chiyani ndalama zanu mukuwonongera zinthu zimene samadya, ndipo mukuwononga malipiro anu pa zinthu zimene sizikhutitsa? Tamverani, mvetsetsani zimene ndikunena kuti mudye zimene zili zabwino; ndipo mudzisangalatse.
3 Open your ears and come to me; listen, that your soul may live. I will make an everlasting covenant with you, my faithful love promised to David. Tcherani makutu ndipo mubwere kwa Ine; mvereni Ine, kuti mukhale ndi moyo. Ndidzachita nanu pangano losatha, chikondi changa chija chosasinthika ndi chodalirika ndinalonjeza Davide.
4 See, I have appointed him a witness to the peoples, a leader and commander of the peoples. Taonani, ine ndamusankha kuti akhale mboni yanga kwa mitundu ya anthu, kuti akhale mtsogoleri ndi wolamulira mitundu ya anthu.
5 Surely you will summon a nation you do not know, and a nation that does not know you will run to you, because of your Father, the Holy One of Israel, for he has glorified you." Ndithu inu mudzayitanitsa mitundu ya anthu imene simuyidziwa, ndipo mitundu ya anthu imene sikudziwani idzabwera ndi liwiro kwa inu. Izi zidzatero chifukwa Yehova Mulungu wanu, Woyerayo wa Israeli, wakuvekani ulemerero.”
6 Seek our Father while he may be found; call on him while he is near. Funafunani Yehova pamene Iye akupezeka. Mupemphere kwa Iye pamene ali pafupi.
7 Let the wicked abandon his way, and the unrighteous man his thoughts. Let him return to our Father, and our Father's heart will be moved with compassion for him; return to our Father, for he will freely pardon. Woyipa asiye makhalidwe ake oyipa, ndipo wosalungama asinthe maganizo ake oyipa. Abwerere kwa Yehova, ndipo adzamuchitira chifundo, ndi kwa Mulungu wathu, pakuti adzamukhululukira koposa.
8 "For my thoughts are not your thoughts, neither are your ways my ways,' declares our Father. “Pakuti maganizo anga siwofanana ndi maganizo anu, ngakhale njira zanu si njira zanga,” akutero Yehova.
9 'For as the heavens are higher than the earth, so are my ways higher than your ways, and my thoughts than your thoughts. “Monga momwe mlengalenga muli kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nʼzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.
10 "For as the rain and the snow come down from heaven and do not return there, but water the earth, making it produce and sprout, giving seed to the sower and bread for those who eat, Monga mvula ndi chisanu chowundana zimatsika kuchokera kumwamba, ndipo sizibwerera komweko koma zimathirira dziko lapansi. Ndipo zimameretsa ndi kukulitsa zomera kenaka nʼkupatsa mlimi mbewu ndi chakudya.
11 so will my word be that goes out from my mouth: it will not return to me empty, but will accomplish what I desire and achieve the purpose for which I sent it. Ndi mmenenso amachitira mawu ochokera mʼkamwa mwanga. Sadzabwerera kwa Ine kopanda phindu lake, koma adzachita zonse zimene ndifuna, ndipo adzakwaniritsa cholinga chimene ndinawatumira.
12 You will go out in joy and be led out in peace; the mountains and the hills will break into singing before you, and all the trees of the field will clap their hands. Inu mudzatuluka mu mzindawo mwachimwemwe ndipo adzakutsogolerani mwamtendere; mapiri ndi zitunda zidzakuyimbirani nyimbo, ndipo mitengo yonse yamʼthengo idzakuwombereni mʼmanja.
13 Instead of the thornbush the cypress will grow, and instead of the brier the myrtle will grow. This will be for the renown of our Father, an everlasting sign that will not be cut off.'" Mʼmalo mʼmene tsopano muli mitengo ya minga mudzamera mitengo ya payini, ndipo kumene kuli mkandankhuku kudzamera mchisu. Zimenezi zidzakhala chikumbutso cha Yehova, ngati chizindikiro chamuyaya, chimene sichidzafafanizika konse.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]