Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 21 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 The oracle of the wilderness of the sea. Like whirlwinds sweeping the Negev, it comes from the wilderness, a fearsome land. Uthenga wonena za chipululu cha mʼmbali mwa Nyanja. Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya adzabwera ngati kamvuluvulu amene akuwomba modutsa mʼmbali ya nyanja, kuchokera ku chipululu, dziko lochititsa mantha.
2 A harsh vision has been shown to me: the betrayer betrays, and the destroyer destroys. Go up, Elam! Lay siege, Media! I have put an end to all the groaning she caused. Ine ndaona zinthu zoopsa mʼmasomphenya: Wonyenga akunyenga, wofunkha akufunkha komanso owononga akuwononga. Elamu, yambani nkhondo! Mediya, zingani mzinda! Ine ndidzathetsa mavuto onse amene anayambitsa Ababuloni.
3 Therefore my body is gripped with anguish; pangs have seized me, like the pangs of a woman in labor. I am too doubled over to hear, too terrified to see. Chifukwa cha zimenezi thupi langa likunjenjemera ndi mantha, ndikumva ululu ngati wa mayi amene akubereka; ndikuvutika kwambiri ndi zimene ndikumva, ndathedwa nzeru ndi zimene ndikuziona.
4 My heart staggers; horror overwhelms me. The twilight I longed for has turned to trembling for me. Mtima wanga ukugunda, ndipo ndikunjenjemera ndi mantha; chisisira chimene ndakhala ndikuchifuna chasanduka chinthu choopsa kwa ine.
5 They set the table, they spread the rugs, they eat, they drink. Rise up, you princes! Oil the shields! Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya akukonza matebulo, akuyala mphasa, akudya komanso kumwa! Mwadzidzidzi anamva mawu akuti, “Dzukani inu ankhondo, pakani mafuta zishango zanu!”
6 For this is what the Sovereign Father said to me: "Go, station the watchman; let him report what he sees. Zimene Ambuye akunena kwa ine ndi izi; “Pita, kayike mlonda kuti azinena zimene akuziona.
7 When he sees riders, horsemen in pairs, riders on donkeys, riders on camels, let him watch closely, very closely." Taonani, anthu akubwera ali pa akavalo ndipo akuyenda awiriawiri, okwera pa bulu kapena okwera pa ngamira, mlondayo akhale tcheru kwambiri.”
8 Then the watchman cried out: "A lion! Upon the watchtower, O Sovereign Father, I stand continually by day, and at my post I keep watch all through the nights." Ndipo mlondayo anafuwula kuti, “Ambuye anga, tsiku ndi tsiku ndimakhala pa nsanja yolondera; Usiku uliwonse ndimakhala pa malo anga olondera.
9 And look—here come riders, horsemen in pairs! And he answered, "Fallen, fallen is Babylon, and all the carved images of her gods lie shattered on the ground." Taonani, uyo munthu akubwera atakwera pa galeta ali ndi gulu la akavalo. Mmodzi wa iwo akuti, ‘Babuloni wagwa, wagwa! Mafano onse a milungu yake agwa pansi ndipo aphwanyika!’ ”
10 O my threshed people, child of my threshing floor, what I have heard from the Father of heaven's armies, I declare to you. Inu anthu anga opunthidwa ndi kupetedwa ngati tirigu, ine ndikukuwuzani zimene ndamva ndikukuwuzani Uthenga wochokera kwa Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli.
11 An oracle about Dumah. Someone calls to me from Seir: "Watchman, what of the night? Watchman, what of the night?" Uthenga wonena za Duma: Munthu wina akundiyitana kuchokera ku Seiri kuti, “Iwe mlonda, usikuwu utha liti? Iwe mlonda, utha liti kodi usikuwu?”
12 The watchman says, "Morning comes, and also the night. If you would inquire, then inquire; come back again." Mlonda akuyankha kuti, “Kukucha, koma kudanso. Ngati ukufuna kufunsa, funsa tsopano; ndipo ubwerenso udzafunse.”
13 The oracle concerning Arabia. In Arabia's thickets you will spend the night, you Dedanite caravans. Uthenga wonena za Arabiya: Inu anthu amalonda a ku Dedani, amene usiku mumagona mʼzithukuluzi za ku Arabiya,
14 Bring water to the thirsty; you who live in the land of Tema, bring bread to the fugitive. perekani madzi kwa anthu aludzu. Inu anthu a ku Tema perekani chakudya kwa anthu othawa nkhondo.
15 For they have fled from the swords—from the drawn sword, from the bent bow, and from the weight of battle. Iwo akuthawa malupanga, lupanga losololedwa, akuthawa uta wokokakoka ndiponso nkhondo yoopsa.
16 For the Sovereign Father told me: "Within a year, as a hired worker counts it, all Kedar's glory ends. Zimene Ambuye akunena kwa ine ndi izi: “Chaka chimodzi chisanathe, potsata mmene amawerengera munthu waganyu, ulemerero wonse wa Kedara udzatheratu.
17 The remaining archers, Kedar's warrior sons, will be few, for our Father has spoken." Mwa anthu okoka uta, ankhondo a ku Kedara opulumuka adzakhala owerengeka.” Wayankhula ndi Yehova Mulungu wa Israeli.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]