Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 22 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 An oracle concerning the Valley of Vision. What is the matter with you now, that you have all gone up to the rooftops, Uthenga wonena za Chigwa cha Masomphenya: Kodi chachitika nʼchiyani, kuti nonsenu mukwere pa madenga?
2 you town full of noise, you wild, chaotic city, you reveling town? Your dead were not killed by the sword, nor did they die in battle. Iwe mzinda wodzaza ndi chisangalalo chodzaza tsaya, iwe mzinda waphokoso ndi wosokonekera? Anthu ako ophedwa aja sanaphedwe ndi lupanga, kapena kufera pa nkhondo.
3 All your rulers fled together; they were captured without a bow being drawn. All of you who were found were taken captive together, though you had fled far away. Atsogoleri ako onse ngakhale anathawa limodzi; koma anagwidwa osadziteteza nʼkomwe. Inu munapezeka ndipo nonse pamodzi munatengedwa ukapolo, ngakhale munathawa pamene mdani akanali patali.
4 So I said, "Look away from me; let me weep bitterly. Do not try to comfort me over the ruin of the daughter of my people." Nʼchifukwa chake Ine ndinati, “Chokani pamaso panga; ndilekeni ndilire ndi mtima wowawa. Musayesere kunditonthoza chifukwa cha kuwonongeka kwa anthu anga.”
5 For the Father of heaven's armies has a day of tumult and trampling and confusion in the Valley of Vision—walls battered down and a cry for help echoing to the mountains. Lero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse walola kuti tione mavuto ndi kugonjetsedwa ndiponso chisokonezo mʼChigwa cha Masomphenya. Malinga agumuka, komanso anthu akanalira mofuwula ku mapiri.
6 Elam took up the quiver with chariots and horsemen, and Kir bared their shields. Ankhondo a ku Elamu anadza pa magaleta ndi akavalo ali ndi mivi mʼmanja. Ankhondo a ku Kiri anakonzeka ndi zishango.
7 Your choicest valleys were full of chariots, and the horsemen took their positions at the gates. Zigwa zanu zachonde ndi zodzaza ndi magaleta, ndipo asilikali okwera pa akavalo ayikidwa pa zipata za mzinda;
8 Our Father stripped away the defenses of Judah. And in that day you looked to the weapons in the House of the Forest, zonse zoteteza Yuda zachotsedwa. Ndipo tsiku limenelo munayangʼanayangʼana zida zankhondo zomwe zinali mʼnyumba yaufumu ya nkhalango;
9 and you saw how many breaches there were in the city of David. You collected the water of the lower pool, inu munaona kuti makoma ambiri a mzinda wa Davide anali ndi malo ambiri ogumuka; munasunga madzi mu chidziwe chakumunsi.
10 and you counted the houses of Jerusalem and tore some down to fortify the wall. Munawerenga nyumba zonse za mu Yerusalemu ndipo munagwetsa nyumba zina kuti mulimbitse linga logumuka lija.
11 You built a reservoir between the two walls for the water of the old pool, but you did not look to the One who made it, nor consider our Father who planned it long ago. Pakati pa makoma awiri munamanga chitsime chosungiramo madzi ochokera ku dziwe lakale, koma inu simunadalire Mulungu amene anapanga zimenezi, kapena kusamalako za Iye amene anazilenga kale lomwe.
12 In that day the Father of heaven's armies called for weeping and mourning, for shaved heads and mourning clothes. Pa tsiku limenelo, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse anakuyitanani kuti mulire ndi kukhetsa misozi; kumeta mutu wanu mpala ndi kuvala ziguduli.
13 But instead there was joy and celebration, slaughtering cattle and killing sheep, eating meat and drinking wine: "Let us eat and drink, for tomorrow we die!" Koma mʼmalo mwake inu munakondwa ndi kusangalala; munapha ngʼombe ndi nkhosa; munadya nyama ndi kumwa vinyo. Inu mumati, “Tiyeni tidye ndi kumwa pakuti mawa tifa!”
14 The Father of heaven's armies has revealed this to me: "Surely this sin will not be wiped away from you until you die," says the Father of heaven's armies. Yehova Wamphamvuzonse wandiwululira mondinongʼoneza kuti, “Tchimo limeneli sindidzakhululuka mpaka tsiku la kufa kwanu,” akutero Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse.
15 This is what the Father of heaven's armies says: Go to this steward, Shebna, who is over the household, and say to him: Chimene Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Pita, ukanene kwa Sabina kapitawo, amene amayangʼanira nyumba yaufumu:
16 What are you doing here, and who gave you the right to be here, that you have cut out a tomb for yourself here—carving your grave high up on the heights, chiseling your resting place in the rock? Kodi ukuchita chiyani kuno, nanga ndani anakupatsa chilolezo kuti udzikumbire manda kuno, kudzikumbira manda pa phiri ndi kudzisemera malo opumulira mʼthanthwe?
17 Look, our Father is about to hurl you away violently, you strong man; he will seize firm hold of you. “Samalira, Yehova watsala pangʼono kukugwira zolimba ndi kukuponya mwamphamvu, iwe munthu wamphamvu.
18 He will wind you up tightly and fling you like a ball into a vast open land. There you will die, and there your splendid chariots will lie—you disgrace to your master's house. Iye adzakukulunga kwambiri ngati mpira ndipo adzakuponyera mʼdziko lalikulu. Kumeneko ndiko ukafere ndipo kumeneko ndiko kudzatsalire magaleta ako. Ndipo udzasanduka wochititsa manyazi nyumba ya mbuye wako.
19 I will depose you from your office, and you will be pulled down from your post. Ine ndidzakuchotsa pa ukapitawo wako ndipo ndidzakutsitsa pa udindo wako.
20 In that day I will summon my servant Eliakim son of Hilkiah, “Tsiku limenelo ndidzayitanitsa mtumiki wanga, Eliyakimu mwana wa Hilikiya.
21 I will clothe him with your robe and fasten your sash on him, and I will hand your authority over to him. He will be a father to the people of Jerusalem and to the house of Judah. Ndidzamuveka mkanjo wako ndi kumangira lamba wako mʼchiwuno mwake ndi kumupatsa ulamuliro wako. Iye adzakhala kholo la amene amakhala mu Yerusalemu ndiponso a fuko la Yuda.
22 I will place the key of the house of David on his shoulder; what he opens no one will shut, and what he shuts no one will open. Ndidzamupatsa ulamuliro wa banja la Davide. Adzatsekula ndipo palibe adzatseke, adzatseka popanda wina kutsekula.
23 I will drive him in like a peg in a firm place, and he will become a seat of honor for his father's house. Ufumu wake udzakhala wokhazikika ngati chikhomo chokhomedwa pa malo olimba. Anthu adzalemekeza nyumba ya abale ake chifukwa cha iye.
24 They will hang on him the whole weight of his father's house—the offspring and the offshoots, every small vessel, from the bowls to all the jars. Ana ndi abale a nyumba ya abambo ake adzakhala ngati katundu pa iye ngati ziwiya zopanda ntchito zimene zapachikidwa pa chikhomo.
25 In that day, declares the Father of heaven's armies, the peg driven into the firm place will give way; it will be cut down and fall, and the load hanging on it will be cut off—for our Father has spoken. “Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Tsiku limeneli chikhomo chokhomedwa kwambiri chija sichidzalimbanso; chidzazuka ndipo chidzagwa ndipo zonse zopachikidwa zidzawonongedwa.’ ” Yehova wayankhula chomwechi.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]